Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/97 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya February
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira February 3
  • Mlungu Woyambira February 10
  • Mlungu Woyambira February 17
  • Mlungu Woyambira February 24
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 2/97 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya February

Mlungu Woyambira February 3

Nyimbo Na. 27

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Bokosi la Mafunso. (“Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita changu kupereka lipoti la utumiki wathu wakumunda mwezi uliwonse?”)

Mph. 15: “Khalani ndi Phande m’Ntchito Imene Sitidzaibwerezanso.” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, phatikizanipo mfundo za m’nkhani yakuti “Keeping on the Watch—How?” pamasamba 714-15 m’buku la Proclaimers.

Mph. 20: “Kulalikira Uthenga Wabwino Mwachangu.” (Ndime 1-5) Atakambapo ndemanga zachidule pandime 1, tcheyamani akambitsirane ndime 2-5 ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu. Apende mfundo zazikulu za maulaliki osonyezedwawo ndi kutchula chifukwa chake maulaliki ameneŵa kapena ena ofanana nawo angakhale ogwira mtima m’gawo lakwawolo. Ofalitsawo asinthane kuyeseza maulalikiwo. Tcheyamani awayamikire, ndi kutchula njira zina zimene zingapangitse maulalikiwo kukhala ogwira mtima kwambiri, ndipo akumbutsa mpingo za kufunika kwa kuchita chopereka chanthaŵi zonse cha K12.00. Ndiyeno apemphe omvetsera kutchula njira zimene angafikire chonulirapo choyambitsa maphunziro. Atchule malingaliro otsimikizika osonyeza mmene angayambire phunziro m’kupita kwa nthaŵi m’buku la Chidziŵitso.

Nyimbo Na. 34 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 10

Nyimbo Na. 29

Mph. 5: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 10: “Kulalikira Uthenga Wabwino Mwachangu.” (Ndime 6-8) Khalani ndi zitsanzo za maulaliki a m’ndime 6-7. Gogomezerani kufunika kwake kopanga ulendo wobwereza watanthauzo kwa amene anasonyeza chidwi.

Mph. 30: “Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho ya woyang’anira utumiki. Tchulani mfundo za m’bokosi lili patsamba 3. Pendani ndandanda zachitsanzo zili patsamba 6. Wofalitsa aliyense wobatizidwa alingalirepo payekha ndiponso mwapemphero ngati akhoza kulembetsa mwezi umodzi kapena yoposapo. Ofalitsa osabatizidwa angafutukule utumiki wawo mwa kudziikira chonulirapo cha maola mwezi ndi mwezi.

Nyimbo Na. 43 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 17

Nyimbo Na. 30

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Tchulani mfundo zosangalatsa zokambitsirana m’magazini atsopano amene mungagwiritsire ntchito mu utumiki mlungu uno.

Mph. 13: “Chikumbutso—Chochitika Chofunika Kwambiri!” Mafunso ndi mayankho. Perekani chilimbikitso cha kuona mwezi wonse wa March kukhala wapadera mwa kuchita upainiya wothandiza.

Mph. 22: Kuyamba Maphunziro a Baibulo Apanyumba. Miyezi yaposachedwa, mabuku azikuto zolimba zikwi mazanamazana agaŵiridwa. Zimenezi zikuyala maziko oyambira maphunziro a Baibulo ena owonjezera. Fotokozani mabuku ndi zofalitsa zina zimene mwagaŵira kwanuko. Limbikitsani ofalitsa kuti abwerere kwa osonyeza chidwi. Pemphani ofalitsa angapo asimbe molunjika khama limene iwo anachita kuti ayambe maphunziro a Baibulo atsopano apanyumba. Gogomezerani mfundo yakuti mbali yofunika kwambiri pantchito yathu ndiyo kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Tingachite zimenezi mogwira mtima ngati tiyesetsa kutsatira malingaliro ofotokozedwa m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996.

Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 24

Nyimbo Na. 32

Mph. 18: Zilengezo zapamalopo. Lengezani maina a onse amene akuchita upainiya wothandiza m’March. Tchulani kuti nthaŵi yopereka fomu yofunsirapo idakalipo. Limbikitsani onse kutengamo mbali mokwanira mu utumiki wakumunda Loŵeruka, March 1. Fotokozani makonzedwe enanso amene akupangidwa pamalopo a kukumana kwa utumiki m’mwezi uno. Lipendeni bwinobwino Bokosi la Mafunso. (“Kodi tiyenera kuchitanji pamene kwagwa tsoka . . .”)

Mph. 12: “Bwanji Nanga za Achibale Anu?” Mwamuna ndi mkazi wake akukambitsirana nkhaniyo pamodzi ndipo asankha njira imene adzafikira nayo achibale osakhulupirira ndi uthenga wabwino.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1990, masamba 25-7.

Mph. 15: Pendani Buku Logaŵira m’March—Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Fotokozani mwachidule chochititsa mabanja kusweka m’chitaganya chamakono. (Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1992, masamba 4-7.) Pendani zamkati mwa bukulo, patsamba 3. Pemphani omvetsera kusankha mitu imene ingakhale maziko a ulaliki. Sonyezani bokosi lophunzitsa lothandiza lopezeka kumapeto kwa mutu uliwonse. Wofalitsa wokhoza achite chitsanzo chogaŵira bukulo. Kumbutsani onse kuwombola makope awo ogwiritsira ntchito mapeto a mlungu uno. Onse ayenera kukumbukira kuti mabuku a mpingo satengedwa pangongole.

Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena