Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/97 tsamba 1
  • Bwanji Nanga za Achibale Anu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Nanga za Achibale Anu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingalalikire Achibale
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Tsitsimulani Achibale Anu ndi Madzi a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Omwe Si Mboni?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Choonadi Sichibweretsa “Mtendere Koma Lupanga”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 2/97 tsamba 1

Bwanji Nanga za Achibale Anu?

1 Ambirife tili ndi achibale ochuluka amene saali m’choonadi. Mmene timafunira kuti okondedwa ameneŵa atsagane nafe panjira ya kumoyo! Ndiponso nkhaŵa yathu kaamba ka mtsogolo mwawo mosatha imakula kwambiri pamene iwo ali a m’nyumba yathu. Ngakhale kuti tayesa zaka zambiri kuwakopa ndi choonadi, sitiyenera kuganiza kuti palibe zimene zidzachitika.

2 Pamene Yesu anali kulalikira, “angakhale abale ake sanakhulupirira Iye.” (Yoh. 7:5) Panthaŵi ina, achibale ake anaganiza kuti wachita msala. (Marko 3:21) Komabe, Yesu sanawalekerere ayi. M’kupita kwa nthaŵi, abale ake analandira choonadi. (Mac. 1:14) Mbale wake wa mimba ina Yakobo anakhala mzati mumpingo wachikristu. (Agal. 1:18, 19; 2:9) Ngati mukufuna kukondwa poona achibale anu akulandira choonadi, musasiye kuyesa kuwafikira ndi uthenga wabwino wa Ufumu.

3 Mukhale Wopumulitsa, Osati Wotopetsa: Pamene Yesu analalikira ena, omvetsera ake anapeza mpumulo, sanaopsezedwe. (Mat. 11:28, 29) Sanawatopetse ndi ziphunzitso zimene iwo sakanatha kumva. Kuti muwapatse mpumulo achibale anu ndi madzi a choonadi, apatseni kapu imodzi nthaŵi imodzi, osati chitini chonse! Woyang’anira woyendayenda wina anati: “Aja amene amadzutsa chidwi mwa achibale awo mwa kuwalalikira pang’onopang’ono amapeza mapindu abwino koposa.” Mwanjira imeneyi, ngakhale otsutsa angayambe kufunsa zambiri ndipo m’kupita kwa nthaŵi angamve ludzu la choonadi.—1 Pet. 2:2; yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:1, 2.

4 Akristu ambiri okwatira alalikira mogwira mtima kwa anzawo a muukwati osakhulupirira mwa kusiya mabuku otseguka pankhani imene ingawakope. Mlongo wina yemwe ankachita zotere ankachitanso phunziro ndi ana ake mwamuna wake akumvetsera pafupi, akumafotokoza zinthu zimene mwamunayo akanapindula nazo. Nthaŵi zina ankafunsa mwamuna wakeyo kuti: “Paphunziro langa lero ndaphunzira zotere. Kodi muganizapo bwanji?” Pomaliza mwamuna wakeyo analandira choonadi.

5 Mukhale Waulemu, Osati Aphuma: Wofalitsa wina ananena kuti “ngakhale achibale ayenera kukhala ndi malingaliro awoawo.” Chotero tiyenera kuwalemekeza pamene anena malingaliro awo kapena pamene atiuza mosapita m’mbali kuti tisamawalankhuze za choonadi. (Mlal. 3:7; 1 Pet. 3:15) Mwa kukhala oleza mtima ndi achikondi ndipo mwa kumvetsera bwino, tingafunefune mipata yoyenera yolalikira mochenjera. Kuleza mtima kotero kumafupa, monga momwe zinachitikira mwamuna wina wachikristu amene anapirira moleza mtima nkhanza ya mkazi wake wosakhulupirira kwa zaka 20. Mkaziyo atangoyamba kusintha, mwamunayo anati: “Mmene ndikumthokozera Yehova kuti wandithandiza kukulitsa kuleza mtima, chifukwa tsopano nditha kuona mapindu ake: Mkazi wanga wayamba kuyenda panjira ya kumoyo!”

6 Bwanji nanga za achibale anu? Zingachitike kuti mwa mayendedwe anu abwino achikristu ndi mwa kuwapempherera iwo, “mungaŵakokere kwa Yehova.”—1 Pet. 3:1, 2, NW, mawu amtsinde.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena