Misonkhano Yautumiki ya May
Mlungu Woyambira May 5
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Loyamba m’Malaŵi.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Asonyezeni Nkhaŵa Yeniyeni Ochita Chidwi Onse Omwe Mwapeza.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Gogomezerani kufunika kwa kubwererako kukakulitsa chidwi cha onse. Longosolani njira zanzeru zopemphera keyala yakunyumba ya omwe timakumana nawo moyenda, kuti tipitirize kuwachitira umboni. Ofalitsa aluso asonyeze zitsanzo ziŵiri zimene zili m’ndime 6-9. Alimbikitseni onse kukonza nthaŵi mlungu uliwonse yopanga maulendo obwereza.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 12
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 12: Kukambitsirana ndi Omvetsera nkhani yakuti ‘Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna,’ yochokera m’kope la Nsanja ya Olonda ya January 15, 1997, masamba 16 ndi 17. Gwiritsirani ntchito mfundozo pamkupiti wapadera wogaŵira brosha la Mulungu Amafunanji m’May.
Mph. 23: “Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza.” (Ndime 1-20) Mafunso ndi mayankho. Mwachidule chitirani chitsanzo ndime 16.
Nyimbo Na. 162 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 19
Mph. 10 Zilengezo zapamalopo ndi Bokosi la Mafunso. Mkulu aikambe.
Mph. 20: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Apanyumba Opita Patsogolo.” Mbale waluso akambitsirane nkhaniyi ndi wofalitsa mmodzi kapena aŵiri amene amachita bwino pochititsa maphunziro. Pogwiritsira ntchito zigawo za buku la Chidziŵitso monga zitsanzo, akulongosola njira zophunzitsira zomwe zimawathandiza kuliyendetsabe Phunzirolo paliŵiro labwino ndi zomwe zimawachititsa kuzindikira zimene wophunzirayo akuphunziradi.—Onani mphatika mu Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, ndime 5, 8, 12, ndi 21.
Mph. 18: “Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza.” (Ndime 21-35) Mafunso ndi mayankho. Pendani bokosi lili patsamba 3. Alimbikitseni onse kuŵerengera maulendo obwereza alionse amene apanga mkati mwa mwezi pamene akupereka lipoti lawo lautumiki wakumunda mwezi uliwonse.
Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 26
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Pendani buku logaŵira m’June. Kugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso, fotokozani mmene mungagwiritsirire ntchito mfundo zili m’ndime 17-19 pamasamba 10-11 kukonza ulaliki wachidule. Alimbikitseni onse kumalingalira zoyamba maphunziro. Gogomezerani kuti ochita chidwi onse tiyenera kuwathandiza kupita patsogolo mwamsanga.—Onani Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, masamba 13-14.
Mph. 12: “Kodi Nchifukwa Ninji Timabwererako?” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mfundo zili m’bokosi patsamba 570, m’buku la Proclaimers.
Mph. 18: Zosoŵa zapamalopo. Nkhani yamkulu kapena akulu aŵiri omakambitsirana zosoŵa zauzimu pampingopo. Perekani uphungu wa m’Malemba ndi malingaliro owongolera zinthu.
Nyimbo Na. 174 ndi pemphero lomaliza.