Bokosi la Mafunso
◼ Ngati ndife mbale tili ndi mlongo mu utumiki wathu, kapenanso tapeza mkazi panyumba tili tokha; kayanso ndife mlongo tili ndi mbale, kapenanso tapeza mwamuna tili tokha, kodi tifunikira kusamala chiyani?
Tili ndi chifukwa chabwino chokhulupirira kuti abale ndi alongo athu amafuna kudzisunga kwambiri pamakhalidwe awo. Komabe, tikukhala m’dziko lonyansa, lololera zoipa lomwe ndi losadziletsa pamakhalidwe ake. Pamene kuli koti tili ndi zolinga zabwino, tiyenera kusamala nthaŵi zonse kuti tipeŵe chitonzo kapena kuchita kanthu kena kosayenera. Zimenezi zikuphatikizapo kusamala pamene tili mu utumiki.
Mu utumiki wakumunda kaŵirikaŵiri abale amapeza akazi kapena alongo kupeza amuna amene amasonyeza chooneka ngati chidwi chenicheni cha choonadi. Ngati pakhomopo tafikapo tokha ndipo mulibenso wina m’nyumbamo, kaŵirikaŵiri zimakhala bwino kwambiri kumlalikira muli pakhomo pompo m’malo moloŵa m’nyumba. Ngati wakondwa nazo, mungakonze kudzabwererako ndi wofalitsa wina kapena pamene ena a m’banjalo aliponso. Ngati zimenezo nzosatheka, kungakhale kwanzeru kumsiya mwini nyumbayo m’manja mwa wofalitsa wina, mkazi kapena mwamuna mnzake. Zilinso choncho ndi mwamuna amene akuphunzira Baibulo ndi mkazi kapena mkazi amene akuphunzira ndi mwamuna.—Mat. 10:16.
Tifunika kusamala pamene tikusankha wina wogwira naye ntchito mu utumiki. Ngakhale kuti ofalitsa, mkazi ndi mwamuna nthaŵi zina angagwire ntchito pamodzi, zimakhala bwino kwambiri ngati ali pagulu. Ngakhale pamene tili mu utumiki, si kwanzeru kutha nthaŵi yaitali tili tokha ndi wina amene sali mkazi wathu kapena mwamuna wathu. Choncho, mbale yemwe akuyang’anira gulu lautumikilo ayenera kusamala pogaŵa ofalitsa, kuphatikizapo achinyamata, kuti agwire ntchito limodzi.
Nthaŵi zonse tikamasamala, tidzapeŵa ‘kudzikhumudwitsa’ tokha kapena anzathu.—2 Akor. 6:3.