Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/97 tsamba 3-6
  • Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Maulendo Obwereza Amathandiza Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 11
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 5/97 tsamba 3-6

Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza

1 Kodi mumasangalala ndi kupanga maulendo obwereza? Ofalitsa ambiri amatero. Mwina poyamba munali wamantha, makamaka pobwerera kwa eni nyumba omwe sanasonyeze chidwi chenicheni polankhula nawo nthaŵi yoyamba. Koma pamene ‘mulimbika mtima mwa Mulungu wathu kulankhula Uthenga Wabwino wa Mulungu’ popanga maulendo obwereza, mungadabwe kuona mmene ntchitoyi ingakhalire yosavuta ndi yopindulitsa. (1 Ates. 2:2) Motani?

2 Kwenikweni, pali kusiyana kofunika kudziŵa pakati pa ulendo wobwereza ndi ulendo woyamba. Ulendo wobwereza timaupanga kwa munthu amene tamdziŵa, osati mlendo, ndipo nkosavuta kwenikweni kulankhula ndi munthu amene tamdziŵa kuposa mlendo. Ponena za mapindu okhutiritsa a kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi, maulendo obwereza angatsegule njira ku maphunziro a Baibulo apanyumba obala zipatso.

3 Pamene tigwira ntchito kunyumba ndi nyumba, mobwerezabwereza timafikira anthu omwe poyamba sanali okondweretsedwa pamene tinawafikira. Nanga nchifukwa ninji timapitiriza kuwafikira? Chifukwa tikudziŵa kuti mikhalidwe ya anthu imasintha ndi kuti munthu yemwe anaoneka wamphwayi kapena wotsutsa poyambapo angakhale wokondweretsedwa pamene timfikiranso. Pokumbukira zimenezo, timakonzekera bwino lomwe ndi kupempherera dalitso la Yehova kuti zimene tidzanena ulendo uno zidzamfike pamtima kuti achitepo kanthu.

4 Ngati pamene tili m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, timafuna kulalikira anthu amene poyamba sanali okondweretsedwa konse, kodi sitiyenera kukhala ofunitsitsa kubwerera kwa aliyense yemwe wasonyeza chidwi pang’ono pa uthenga wa Ufumu?—Machitidwe 10:34, 35.

5 Ambirife tili m’choonadi lero chifukwa chakuti wofalitsa wina analeza mtima napanga maulendo obwereza kwa ife. Ngati muli mmodzi wa ameneŵa, mungadzifunse kuti: ‘Kodi poyamba ndinapereka chithunzi chotani kwa wofalitsa uja? Kodi ndinalandira uthenga wa Ufumu pomwepo nditaumva nthaŵi yoyamba? Kodi mwina ndinaoneka wamphwayi?’ Tiyenera kukhala wokondwera kuti wofalitsa yemwe anabwereranso kwa ife anatiyesa woyenera ulendo wobwereza, ‘nalimbika mtima mwa Mulungu,’ natifikira, ndi kupitiriza kutiphunzitsa choonadi. Bwanji za aja omwe amasonyeza chidwi poyamba komano pambuyo pake nkumayesa kutipeŵa? Tiyenera kukhala ndi maganizo abwino, monga momwe chochitika chotsatirachi chikusonyezera.

6 Tsiku lina mmaŵa pamene ofalitsa aŵiri anali mu umboni wa m’khwalala, anakumana ndi mkazi wachitsikana alikukankha mwana m’pulemu. Mkaziyo analandira magazini naitanira alongowo kunyumba kwake Sande yotsatira. Iwo anakafika panthaŵi yomwe analonjezanayo, koma mwini nyumbayo anawauza kuti analibe nthaŵi yoti akambitsirane. Komabe, analonjeza kuti adzakambitsirana nawo mlungu wotsatira. Alongowo anakayikira ngati kuti adzasunga panganolo, koma atabwererako anapeza kuti mkaziyo anali kuwadikira. Phunziro linayambidwa, ndipo mkaziyo anapita patsogolo modabwitsa. Posapita nthaŵi, anayamba kufika kumisonkhano mokhazikika ndi kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Tsopano ndi wobatizidwa.

7 Yalani Maziko Paulendo Woyamba: Maziko a ulendo wobwereza wachipambano kaŵirikaŵiri amayalidwa paulendo woyamba. Mvetserani mosamala zonena za mwini nyumba. Kodi zikusonyezanji kwa inu? Kodi ndi wopembedza? Kodi ali wodera nkhaŵa ndi nkhani za mikhalidwe ya zinthu? Kodi amakonda sayansi? mbiri yakale? malo otizinga? Kumapeto kwa ulendo wanu, mungadzutse funso lochititsa kulingalira ndi kulonjeza kudzakambitsirana naye yankho la m’Baibulo pamene mubweranso.

8 Mwachitsanzo, ngati mwini nyumba avomereza lonjezo la m’Baibulo la dziko lapansi laparadaiso, mungadzapitirize kukambitsirana nkhaniyo. Musanachoke, mungafunse kuti: “Kodi tingatsimikize motani kuti Mulungu adzakwaniritsadi lonjezo limeneli?” Ndiyeno wonjezani kuti: “Mwinamwake ndingadzerepo pamene onse m’banja ali panyumba kuti ndidzakusonyezeni yankho la m’Baibulo pa funso limeneli.”

9 Ngati mwini nyumbayo sanasonyeze chidwi pankhani iliyonse, mungadzutse limodzi la mafunso osonyezedwa patsamba lakumbuyo kwa Utumiki Wathu Waufumu ndi kuligwiritsira ntchito monga maziko a kukambitsirana kwanu paulendo wotsatira.

10 Khalani ndi Cholembapo Cholondola: Cholembapo chanu cha kunyumba ndi nyumba chiyenera kukhala cholondola ndi chokwanira. Lembani dzina ndi keyala ya mwini nyumba mutangochoka pakhomo. Musalotere nambala ya nyumba kapena dzina la msewu—pendaninso zimene mwalemba kutsimikiza kuti nzolondola. Lembani chizindikiro cholongosola munthuyo. Lembani nkhani imene mwakambitsirana, malemba omwe munaŵerenga, buku lililonse limene munasiya, ndi funso limene mudzayankha pobwererako. Phatikizanipo tsiku ndi nthaŵi ya ulendo woyamba ndi pamene mwalonjeza kuti mudzabweranso. Pakuti tsopano cholembapo chanu chakwanira, musachitaye! Chiikeni pamalo osungika pamene mungachipeze mukadzachifuna. Pitirizani kulingalira za munthuyo ndi mmene mudzachitira paulendo wotsatira.

11 Dziŵani Zolinga Zanu: Choyamba, yesani kumasula mwini nyumbayo mwakukhala wachikondi ndi waubwenzi. Sonyezani kuti muli ndi chidwi mwa iye monga munthu, popanda kuchita chizoloŵezi chopambanitsa. Kenako, mukumbutseni za funso lililonse limene munadzutsa paulendo wapita. Mvetserani mosamalitsa lingaliro lake, ndipo yamikirani moona mtima zonena zake. Ndiyeno, sonyezani chifukwa chake lingaliro la Baibulo lili lothandiza. Ngati kuli kotheka, msonyezeni lingaliro logwirizana nalo m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kumbukirani kuti cholinga chanu chachikulu pamaulendo obwereza ndicho kuyambitsa phunziro la Baibulo.

12 Kulunjika kwa buku la Chidziŵitso kwasonkhezera ambiri a ife ‘kulimbika mtima’ pa maphunziro a Baibulo kulimbikitsa ophunzirawo kufika pamisonkhano ndi kuyanjana ndi gulu la Yehova. Kale, tinkayembekezera kufikira anthu ataphunzira kwa nthaŵi yaitali ndithu tisanawaitanire kudzayanjana nafe. Tsopano, maphunziro ambiri amafika pamisonkhano atangoyamba kuphunzira, ndipo chifukwa cha zimenezo amapita patsogolo mwamsanga kwambiri.

13 Mbale ndi mkazi wake analalikira mwamwaŵi kwa mnzawo wakuntchito. Pamene anasonyeza chidwi pa choonadi, anampempha kuphunzira naye buku la Chidziŵitso. Panthaŵi imodzimodziyo, anamuuza kuti ayenera kumapita kumisonkhano, kumene mayankho ake ambiri akhoza kuyankhidwa. Mwamunayo sanangovomereza chiitano chawo mofunitsitsa komanso anayamba kufika pamisonkhano mokhazikika ku Nyumba ya Ufumu.

14 Gwiritsirani Ntchito Brosha Lakuti Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife?: Pa Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu,” tinalandira brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Broshali nlothandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo kwa anthu oopa Mulungu mosasamala kanthu kuti anaphunzira motani. Lili ndi kosi yophunzira yotsatirika bwino, yophunzitsa ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Chofalitsachi chidzakhala chiŵiya chothandiza kwambiri chopatsira chidziŵitso chonena za Mulungu. Chimalongosola choonadi momvekera bwino kwambiri ndi mosavuta kwakuti aliyense wa ife adzakhoza kuchigwiritsira ntchito kuphunzitsira ena zimene Mulungu amafuna. Mwachionekere, ofalitsa ambiri adzakhala ndi mwaŵi wa kuchititsa maphunziro a Baibulo m’broshali.

15 Anthu ena omwe amaona kuti alibe nthaŵi yophunzira buku la Chidziŵitso angavomere kumaphunzira mwachidule brosha lakuti Mulungu Amafunanji. Adzasangalala ndi zimene adzaphunzira! Atangophunzira masamba aŵiri kapena atatu, adzadziŵa mayankho a mafunso omwe anthu awasinkhasinkha zaka mazana ambiri: Kodi Mulungu Ndani? Kodi Mdyerekezi Ndani? Kodi Chifuno cha Mulungu Nchiyani Ponena za Dziko Lapansi? Kodi Ufumu wa Mulungu Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani Chipembedzo Choona? Ngakhale kuti broshalo limaphunzitsa choonadi m’mawu osavuta, uthenga wake ngwamphamvu kwambiri. Limafotokoza mfundo zazikulu zimene akulu adzakambitsirana ndi ofunsira ubatizo ndipo lingakhale ulalo wabwino woolokera ku phunziro lokwanira bwino m’buku la Chidziŵitso.

16 Kuti mupemphe kuchita naye phunziro paulendo wobwereza, mungangonena kuti: “Kodi mukudziŵa kuti pamphindi zoŵerengeka chabe mungapeze yankho pa funso lofunika kwambiri la m’Baibulo?” Ndiyeno, funsani funso limene lili kuchiyambi cha limodzi la maphunziro m’broshali. Mwachitsanzo, ngati mwafikira munthu wokalamba, munganene kuti: “Tikudziŵa kuti kale Yesu anachiritsa anthu. Koma kodi nchiyani chimene Yesu mtsogolomu adzachitira odwala? okalamba? akufa?” Mayankho akupezeka m’phunziro 5. Munthu wopembedza angakopeke ndi funso lakuti: “Kodi Mulungu amamva mapemphero onse?” Likuyankhidwa m’phunziro 7. A m’banja angafune kudziŵa pafunso lakuti: “Kodi Mulungu Amafunanji kwa makolo ndi ana?” Angapeze yankho pamene aphunzira phunziro 8. Mafunso ena ndi aŵa: “Kodi akufa angavulaze amoyo?” loyankhidwa m’phunziro 11; “Kodi nchifukwa ninji pali zipembedzo zambiri zimene zimati nzachikristu?” loyankhidwa m’phunziro 13; ndi lakuti “Kodi muyenera kuchitanji kuti mukhale bwenzi la Mulungu?” loyankhidwa m’phunziro 16.

17 Athandizeni Aja Olankhula Chinenero China: Bwanji za eni nyumba olankhula chinenero china? Ngati kuli kotheka, ayenera kuphunzitsidwa m’chinenero chimene adziŵa bwino kwambiri. (1 Akor. 14:9) Woyang’anira dera angadziŵitse mpingo uliwonse za mipingo ya chinenero china m’deralo. Mwa kungoyang’ana mpambowo, mlembi angathe kutumiza kumpingo wachinenero choyenera masilipi a S-70 omwe amalandira kuchokera kuziŵalo zampingo. Ameneŵa sayenera kutumizidwa ku Sosaite. Ngati palibe mipingo kapena magulu apafupi ndipo palibe ofalitsa akumaloko omwe angathe kulankhula chinenero cha mwini nyumbayo, wofalitsa angayese kuphunzira ndi mwini nyumbayo, mwa kugwiritsira ntchito brosha lakuti Mulungu Amafunanji m’zinenero ziŵirizo.

18 Wofalitsa wolankhula Chingelezi anayambitsa phunziro kwa mwamuna wina wolankhula Chiviyetinamu ndiponso ndi mkazi wake, wolankhula Chitai. Paphunzirolo anagwiritsira ntchito zofalitsa ndi ma Baibulo a Chingelezi, Chivietinamu, ndi Chitai. Ngakhale kuti kusiyana chinenero kunali vuto poyamba, wofalitsayo akulemba kuti: “Mwamunayo ndi mkazi wake apita patsogolo mwauzimu mofulumira. Iwo aona kufunika kwa kufika pamisonkhano pamodzi ndi ana awo aŵiri, ndipo amaŵerenga Baibulo usiku uliwonse monga banja. Mtsikana wawo wazaka zisanu ndi chimodzi ali ndi phunziro la Baibulo lakelake.”

19 Pophunzira ndi anthu olankhula chinenero china, lankhulani pang’onopang’ono, tchulani bwinobwino mawu, ndipo gwiritsirani ntchito mawu osavuta. Komabe, kumbukirani kuti anthu olankhula chinenero china tiyenera kuwachitira ulemu. Sitiyenera kuwachita monga makanda.

20 Gwiritsirani ntchito bwino zithunzi zokongolazo m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji. “Ngati chithunzi chimalankhula mawu chikwi chimodzi,” zithunzi zambirimbiri m’broshalo zidzalankhula nkhaninkhani za mawu kwa mwini nyumbayo. Mpempheni kuti aŵerenge malemba m’Baibulo lake. Ngati phunzirolo lingachitidwe pamene wina wa m’banjalo alipo wodziŵa Chicheŵa ndi wokhoza kumasulira, zingakhale zopindulitsa kwambiri.—Onani Utumiki Wathu Waufumu, May 1984, tsamba 8; October 1990, masamba 7-8.

21 Pangani Maulendo Obwereza Mosachedwa: Kodi muyenera kuyembekezera kwa nthaŵi yaitali motani kuti mupange ulendo wobwereza? Ofalitsa ena amabwererako patapita tsiku limodzi kapena aŵiri pambuyo pa ulendo woyamba. Ena amabwererako tsiku lomwelo! Kodi nkufulumira kwambiri? Kwenikweni, eni nyumba ambiri samakana ayi. Kaŵirikaŵiri amakhala wofalitsa amene afunikira kukhala ndi maganizo abwino ndi kulimbikanso mtima pang’ono. Talingalirani zochitika zotsatirazi.

22 Tsiku lina, wofalitsa wazaka 13 anali kulalikira kunyumba ndi nyumba pamene anaona akazi aŵiri alikuyenda pamodzi. Pokumbukira chilimbikitso cha kulalikira kwa anthu kulikonse kumene tiwapeza, anafikira akaziwo pakhwalalapo. Iwo anasonyeza chidwi pauthenga wa Ufumu, ndipo aliyense analandira buku la Chidziŵitso. Mbale wachichepereyo analemba makeyala awo, nabwererako patapita masiku aŵiri, ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo kwa aliyense wa iwo.

23 Mlongo wina amalonjeza kubwererako mlungu wotsatira. Koma patapita tsiku limodzi kapena aŵiri pambuyo pa ulendo wake woyamba, amadzerapo kuti apatse mwini nyumbayo magazini yonena za nkhani imene anakambitsirana poyambapo. Amauza mwini nyumbayo kuti: “Ndaona nkhaniyi ndi kuganiza kuti mungakonde kuiŵerenga. Sitidzakambitsirana lero, koma ndidzafika Lachitatu masana malinga ndi pangano lathu. Kodi nthaŵi ija idakali bwino kwa inu?”

24 Pamene munthu asonyeza chidwi pa choonadi, timadziŵa kuti adzakumana ndi chitsutso mwa njira inayake. Kubwererako kwathu mwamsanga pambuyo pa ulendo woyamba kudzamlimbikitsa kupirira chitsutso chilichonse chimene chingachokere kwa achibale, mabwenzi apamtima, ndi ena.

25 Kulitsani Chidwi cha Aja Opezeka M’malo Apoyera: Ambirife timasangalala kulalikira m’makwalala, m’malo oimika magalimoto, m’zoyendera za onse, m’malo ogulitsira, m’mapaki, ndi m’malo ena otero. Kuwonjezera pa kugaŵira mabuku, tiyenera kukulitsa chidwi. Ndi cholinga chimenecho, tiyenera kuchita khama la kutenga dzina, keyala, ndipo ngati kuli kotheka ndi nambala ya foni yomwe kwa munthu aliyense amene tikumana naye amene wachita chidwi. Kupeza zimenezi sikovuta monga momwe mungaganizire. Pamene makambitsirano akufika kumapeto, tulutsani kabuku kanu ndi kufunsa kuti: “Kodi pali njira iliyonse imene tingapitirizire kukambitsiranaku nthaŵi ina?” Kapena nenani kuti: “Ndingakonde kuti muŵerenge nkhani ina imene ndikhulupirira kuti mudzaikonda. Kodi ndingakubweretsereni kunyumba kapena kuofesi kwanu?” Mbale wina amangofunsa kuti: “Kodi ndingakuimbireni foni panambala iti?” Iye akunena kuti pamiyezi itatu anthu onse anampatsa mwaufulu manambala awo a foni kusiyapo atatu chabe.

26 Gwiritsirani Ntchito Telefoni Kupeza Chidwi ndi Kuchikulitsa: Mlongo wachipainiya amagwiritsira ntchito telefoni kufikira anthu okhala m’nyumba za malinga aatali. Amapanganso maulendo obwereza mwa njira imodzimodziyo. Paulendo woyamba amati: “Ndidziŵa kuti simundidziŵa ine. Ndikuyesa kulankhula ndi anthu kwanu kuno za lingaliro la m’Baibulo. Ngati mungakonde, ndingakondwe kukuŵerengerani pamphindi zochepa lonjezo lopezeka pa . . .” Ataŵerenga lembalo, amati: “Kodi sikungakhale kosangalatsa ngati nthaŵiyo ingafike? Ndakhala wokondwa kwabasi kukuŵerengerani zimenezi. Ngati inunso mwakondwa nazo, ndingakonde kudzaimbanso kuti tikambitsiranenso lemba lina.”

27 Patelefoni ya ulendo wobwereza, amakumbutsa mwini nyumbayo zimene anakambitsirana ulendo wapita ndi kunena kuti akufuna kuŵerenga m’Baibulo mmene mikhalidwe idzakhalira pamene zoipa zidzachotsedwa. Kenako amakambitsirana mwachidule ndi mwini nyumbayo za m’Baibulo. Pakukambitsirana ndi anthu ambiri patelefoni, anthu 35 amuitana kupita kunyumba kwawo ndipo wayambira maphunziro a Baibulo asanu ndi aŵiri! Kodi nkovuta kwa inu kupanga maulendo obwereza kwa anthu okondwerera chifukwa cha matenda kapena zochitika zadzidzidzi? Ngati ndi choncho, bwanji osakambitsirana nawo patelefoni?

28 Kulitsani Chidwi Chimene Mupeza m’Malo Amalonda: Kugwira ntchito kusitolo ndi sitolo kumaloŵetsamo zambiri kuposa kungogaŵira magazini chabe. Ogulitsa m’sitolo ambiri amakhala ndi chidwi chenicheni pa choonadi, ndipo chidwi chimenecho tiyenera kuchikulitsa. Nthaŵi zina, kungakhale kotheka kukambitsirana za m’Baibulo kapena ngakhale kuphunzirira pompo pamalo amalonda. Nthaŵi zina, inu ndi munthu wokondweretsedwayo mungakumane pakupuma kwa masana kapena panthaŵi iliyonse yoyenera.

29 Woyang’anira woyendayenda wina anafikira mwini sitolo yaing’ono ndipo anapempha kumsonyeza chitsanzo cha kachitidwe ka phunziro la Baibulo. Atafunsidwa za utali umene chitsanzocho chidzatenga, woyang’anira woyendayenda anati chidzatenga mphindi 15 zokha. Pakumva zimenezo, mwini sitoloyo anaika chizindikiro pachitseko chonena kuti: “Ndibwera m’Mphindi 20,” anatenga mipando iŵiri, ndipo aŵiriwo anakambitsirana ndime zoyambirira zisanu za m’buku la Chidziŵitso. Mwamuna woona mtima ameneyu anakopeka ndi zimene anaphunzira kwakuti anafika pa Msonkhano Wapoyera ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda pa Sande mlunguwo ndipo anavomera kupitiriza phunziro mlungu wotsatira.

30 Pogaŵira phunziro m’malo amalonda, munganene izi: “Timatenga mphindi 15 zokha kusonyeza mmene timaphunzirira Baibulo. Ngati pali bwino, ndingakonde kukusonyezani mmene timachitira.” Ndiyeno, sungani nthaŵiyo. Ngati sikotheka kukambitsirana kwa nthaŵi yaitali pamalo amalonda, ndi bwino kufikira wogulitsa m’sitoloyo kunyumba kwake.

31 Bwererani Ngakhale Kumene Simunasiyeko Buku Lililonse: Chidwi chilichonse chosonyezedwa chimafunikira ulendo wobwereza, kaya tinagaŵira buku kapena ayi. Komabe, ngati nkoonekeratu kuti mwini nyumbayo sakufuna uthenga wa Ufumu, ndi bwino kupereka chisamaliro chanu kwa anthu ena.

32 M’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, mlongo wina anakumana ndi mkazi yemwe anali waubwenzi kwambiri koma yemwe anakana kwa mtu wa galu kulandira magazini. Wofalitsayo akulemba kuti: “Pamasiku angapo ndinalingalira za iye ndipo ndinaganiza zolankhulanso naye.” Potsirizira pake, mlongoyo anapemphera, nalimbika mtima, ndipo anakagogoda pakhomo pa mkaziyo. Anakondwa kuona kuti mwini nyumbayo anamuitana kuti aloŵe. Phunziro la Baibulo linayambika, ndipo analichitanso mlungu wotsatira. M’kupita kwa nthaŵi, mwini nyumbayo anabwera m’choonadi.

33 Konzekerani Pasadakhale Kuti Muchite Zopambana: Timalimbikitsidwa kuti mlungu ndi mlungu tithere nthaŵi ina m’maulendo obwereza. Tingachite zochuluka ngati tikonzekera bwino. Linganizani kubwerera kwa anthu a m’deralo limene mudzagwiramo ntchito kunyumba ndi nyumba.

34 Aja amene akhala achipambano pakupanga maulendo obwereza ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba akunena kuti nkofunika kusonyeza chidwi chenicheni mwa anthu ndi kupitiriza kuwalingalira ngakhale pambuyo pa ulendo wathu. Nkofunikanso kukhala ndi nkhani yokopa ya m’Baibulo yokambitsirana ndi kuyala maziko a ulendo wobwereza musanachoke paulendo woyamba. Ndiponso, nkofunika kubwerera mwamsanga kukakulitsa chidwi chija. Nthaŵi zonse tikumbukire cholinga cha kuyambitsa phunziro la Baibulo.

35 Mkhalidwe wofunika pa kupanga ulendo wobwereza ndiwo kulimbika mtima. Kodi timakupeza motani? Mtumwi Paulo akuyankha mwa kunena kuti ‘tilimbika mtima’ kuti tilalikire uthenga wabwino kwa ena ‘mwa Mulungu wathu.’ Ngati mukufuna kukula pambali imeneyi, pemphererani thandizo la Yehova. Ndiyeno, mogwirizana ndi mapemphero anu, kulitsani chidwi chilichonse. Yehova adzadalitsadi zoyesayesa zanu!

[Bokosi patsamba 3]

Mmene Mungakhalire Achipambano pa Kupanga Maulendo Obwereza

■ Sonyezani chidwi chanu chenicheni mwa anthu.

■ Sankhani nkhani yokopa ya m’Baibulo yokambitsirana.

■ Yalani maziko a ulendo wobwereza wotsatira uliwonse.

■ Pitirizani kulingalira za munthuyo mutachoka.

■ Bwererani pambuyo pa tsiku limodzi kapena aŵiri kukakulitsa chidwi.

■ Kumbukirani kuti cholinga chanu ndicho kuyambitsa phunziro la Baibulo.

■ Pemphererani thandizo kuti mulimbike mtima pochita ntchitoyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena