Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 11
Kuthandiza Ophunzira Kupanga Maulendo Obwereza
1 Wophunzira Baibulo akayamba kuchita nawo ntchito yolalikira, amakumana ndi anthu amene amachita chidwi ndi uthenga wabwino. Ndiyeno kodi tingam’thandize bwanji wofalitsa watsopano kuchita maulendo obwereza ogwira mtima ndiponso kukulitsa chidwi chimene wapeza?
2 Kukonzekera ulendo wobwereza kumayambira paulendo woyamba. Muyenera kulimbikitsa wophunzirayo kukhala ndi chidwi kwambiri ndi anthu amene walankhula nawo. (Afil. 2:4) M’phunzitseni pang’onopang’ono zimene angachite kuti anthu amene akulankhula nawo azifotokoza maganizo awo, mmene angamvetserere ndemanga zawo, ndiponso mmene angadziwire zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa. Ngati munthu wina wasonyeza chidwi, muuzeni wofalitsa watsopanoyo kulemba zinthu zofunika zokhudzana ndi zimene mwakambirana ndi munthuyo pa ulendo umenewo. Ndiyeno gwiritsani ntchito zimene analembazo kumuthandiza kukonza zoti mukakambirane paulendo wotsatira.
3 Kukonzekera Ulendo Wobwereza: Choyamba, onani zimene munakambirana pa ulendo woyamba, ndipo mukatero m’sonyezeni wophunzirayo mmene angasankhire mfundo ya uthenga wa Ufumu imene ingakasangalatse mwininyumba uja. (1 Akor. 9:19-23) Konzekerani limodzi ulaliki wachidule wokhala ndi lemba limodzi la m’Baibulo ndiponso ndime imodzi kuchokera m’buku logwiritsa ntchito kuchitira phunziro. Kuwonjezera pamenepo, konzani funso limene mukhoza kukafunsa kumapeto kwake kuti mudzapeze poyambira ulendo wotsatira. M’sonyezeni wofalitsa watsopanoyo zimene angachite kuti pa ulendo wobwereza uliwonse azikathandiza munthuyo kudziwa zowonjezereka za Mawu a Mulungu.
4 Ndi bwinonso kuthandiza wophunzira kudziwa mawu oyambira osavuta. Pambuyo popereka moni kwa mwininyumba, anganene kuti: “Ndinasangalala kwambiri ndi mmene tinachezera pa ulendo wapita uja, ndipo ndabweranso kuti ndikambirane nanu zina zochokera m’Baibulo pankhani ya [tchulani nkhani yakeyo].” Muyeneranso kuuza wophunzira watsopano zimene angachite ngati pakhomopo wapezapo munthu wina wosiyana ndi amene amamufuna.
5 Aziyesetsa Kubwererako: M’limbikitseni wophunzirayo kusonyeza chitsanzo chabwino chobwereranso mofulumira kwa onse amene anachita chidwi. Kuti tipeze anthu m’makomo, tingafunike kuchita khama kubwererako. M’phunzitseni wophunzirayo mmene angamapanganirane ndi anthu kuti akabwerenso, ndiponso m’thandizeni kuona kufunika kobwererako mogwirizana ndi mmene analonjezerana. (Mat. 5:37) M’phunzitseni wofalitsa watsopanoyo kukhala wokoma mtima, woganizira ena, ndiponso waulemu pamene akufunafuna anthu onga nkhosa ndi kukulitsa chidwi chawo.—Tito 3:2.