Bokosi la Mafunso
◼ Kodi mumafunikira kalata yokudziŵikitsani?
Ndime yoyamba ya Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu Waufumu wa February 1991 inati: “Mwamsanga pamene wofalitsa wafika kuchokera ku mpingo wina, mlembi wa mpingowo ayenera kutenga kwa wofalitsayo dzina la mpingo wake wakale ndi dzina ndi keyala ya mlembi wa mpingowo. Ndiyeno ayenera kulembera mlembi wa mpingo wakalewo, akupempha khadi la Mpingo Lolembapo la Wofalitsa ndi kalata yomdziŵikitsa. Mlembi wolandira pempholi ayenera kuyankha mofulumira.—Onani Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 104-5.”
Kulemba makalata odziŵikitsa ofalitsa amene sanasamukire kumpingo wina koma apita chabe kukacheza kwa masiku ochepa kapena milungu yochepa sikofunikira. Kuchita zimenezi kumangopatsa mlembi wampingo ntchito yosafunika. Zisamachitike. Wofalitsa amene akusamuka sapatsidwa kalata yomdziŵikitsa, koma imatumizidwa kumpingo watsopanowo pamodzi ndi Khadi la Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo pamene laitanitsidwa ndi mlembi wampingowo.
Pazochitika zoti munthu wodzinenera kukhala wa Mboni za Yehova wabwera m’mpingo kudzafuna chithandizo chakuthupi, akulu ayenera kusamalira nkhaniyo. Uphungu wothandiza posamalira nkhani yoteroyo unaperekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu wa February 1994, tsamba 7, m’nkhani yakuti “Samalani ndi Kukoma Mtima Kolakwika.”