Misonkhano Yautumiki ya January
Mlungu Woyambira January 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Kuthandiza Ena Kuzindikira Phindu la Mabuku Athu.” Mafunso ndi mayankho. Tchulani mabuku akale amene mpingo wanu uli nawo. Fotokozani mmene tingakonzere ulaliki kotero kuti tithe kunena za mfundo yakutiyakuti imene ili m’buku limene tikugwiritsa ntchito. Limbikitsani onse kugaŵira mabuku amenewa mu utumiki wakumunda ndi pochitira umboni mwamwayi mu January.
Mph. 20: “Sonyezani Kuti Mukulimbika pa ‘Kusala Mwazi’” (Mac. 15:28, 29). Ikambidwe mwa mafunso ndi mayankho ndi mkulu woyeneretsedwa.
Nyimbo Na. 61 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Lengezani makonzedwe a utumiki wakumunda a January.
Mph. 20: “Chimene Tasankha—Kulondola Njira ya Moyo ya Yehova.” Nkhani. Wonjezanipo kulimbikitsa onse kuti azifika mokhazikika pamisonkhano isanu ya mlungu uliwonse ya mpingo.
Mph. 15: “Lezani Mtima.” Banja likukambirana. Aonenso njira zimene angakhalire oleza mtima kwambiri mu utumiki wawo. Phatikizanipo ndemanga zoyenerera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1995, tsamba 12.
Nyimbo Na. 135 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 18
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Kusamalira Thupi Lanu.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu woyeneretsedwa. Gogomezerani kuti aliyense ayenera kumvera uphunguwo kaamba ka ubwino wake.
Mph. 10: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo.” Nkhani yokambidwa ndi wochititsa phunziro la buku wachitsanzo chabwino, amene alongosole ntchito yake. Asonyeze mmene ntchitoyo imathandizira mpingo kupita patsogolo ndi kuyendanso bwino mwauzimu. Wonjezanipo mfundo zikuluzikulu za mu buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 43-5, 74-6.
Mph. 15: “Kuyambitsa Maphunziro m’Bolosha la Mulungu Amafunanji.” Kukambirana kwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 25
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo.
Mph. 15: “Kusintha Maola Ofunika kwa Apainiya.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Yamikirani apainiya mu mpingo wanu, ndipo limbikitsani ofalitsa owonjezereka kuti achite utumiki waupainiya wothandiza ndi wokhazikika, akumakumbukira kuti m’miyezi ya March, April, ndi May kuli ntchito yapadera. Wonjezeranipo chidziŵitso chimene chili mu mphatika za Utumiki Wathu Waufumu wa February 1997 ndi July 1998.
Mph. 15: Kodi Mukusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Chaka chilichonse Sosaite imatulutsa kabuku ka Kusanthula Malemba. Kodi inuyo panokha kapena monga banja mumakagwiritsa ntchito bwino kabuku kameneka? Fotokozani zifukwa zopindulitsa zimene tiyenera kumalingalira za lemba la tsiku lililonse. Kambiranani ndemanga zomwe zili mu mawu oyamba a Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1999, masamba 3-4. Funsani ofalitsa kuti alongosole zimene iwo mwapadera akuchita kuti azilingalira lemba latsiku lililonse ndi ndemanga yake monga munthu payekha ndiponso mabanja.
Nyimbo Na. 225 ndi pemphero lomaliza.