Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo
1 Ndi mwayi waukulu kwambiri kuti mkulu kapena mtumiki wotumikira woyeneretsedwa azitumikira monga wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo. Ndi udindo waukulu kuthandiza anthu a m’gulu lake kupeza zimene amasoŵa mwauzimu. Ntchito yake ndi yambali zitatu.
2 Kuphunzitsa Kwaluso: Pamafunika kukonzekera kwambiri kuti wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo mlungu uliwonse azithandiza gululo kuzindikira zinthu. Amayesayesa kuwathandiza kumvetsetsa ndithu nkhani imene akuphunzira. M’malo moti iyeyo aziikapo ndemanga kwambiri panthaŵi yophunzirayo, amafunsa mafunso owonjezera oyenerera kuti anthu atulutse mfundo zikuluzikulu za m’phunzirolo pamene kuli kofunika kutero. Chimene iye amafuna ndi kupangitsa phunzirolo kukhala losangalatsa ndi lolangiza ndinso kuti aliyense azilankhulapo. Cholinga chake ndi kumangirira mwauzimu, kusonyeza mmene phunzirolo lingagwiritsidwe ntchito, ndi kupangitsa nkhaniyo kukhudza maganizo a anthu ndi kuwafika pamtima.—1 Ates. 2:13.
3 Ubusa Wothandiza: Wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ali “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.” (Yes. 32:2) Amasamaliladi anthu onse amene ali m’gulu lake ndipo amaonetsetsa kuti akuwathandiza mwauzimu pamene wina mwa anthu amene akuwayang’anira wakhumudwa.—Ezek. 34:15, 16; 1 Ates. 2:7, 8.
4 Kulalikira Mwachangu: Wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ndi watcheru popanga makonzedwe othandiza kuti onse amene ali m’gulu lake azitha kupita nawo mu utumiki wakumunda mokwanira. Amatsogolera ntchito yolalikira, pozindikira kuti akamalalikira nthaŵi zonse, anthu ena onse a m’gulu lake nawonso adzatengera changu chake ndi chimwemwe chake mu utumiki. (Akol. 4:17; 2 Ates. 3:9) M’kupita kwa nthaŵi, amayesetsa kuti agwirepo ntchito mu utumiki ndi munthu aliyense amene ali m’gulu lake. Ngati tikufuna kunola maluso athu a kulalikira ndi kuphunzitsa mu utumiki, wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo angatithandize kukwaniritsa cholinga chathucho.—1 Tim. 4:16; 2 Tim. 4:5.
5 Tilidi odala chifukwa tili ndi mphatso mwa amuna amene amakhala okonzeka kutithandiza mwauzimu ndi kutichirikiza mwachikondi. (1 Ates. 5:14) Tiyenitu tisonyeze kuti tikuyamikira zinthu zabwino zimene Yehova wapereka mwa kufika nthaŵi zonse paphunziro la buku ndi kuchirikiza mokhulupirika ntchito yolalikira.—Aheb. 10:25.