Chitirani Umboni Choonadi
1 Yesu ananena momveka bwino kuti anabwera padziko lapansi kudzachitira umboni choonadi. Iye anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.”—Yoh. 18:37.
2 Mwa kulalikira kwake mwachangu, Yesu analemekeza dzina la Yehova. Anasonyezanso kuti amakonda anthu pozindikira mkhalidwe wawo wauzimu womvetsa chisoni. Ponena za ntchito yake Mateyu analemba kuti: “Ndipo Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo . . . Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mat. 9:35, 36) Mofanana ndi Yesu, kudzipereka kwathu kwa Yehova pamodzi ndi kukonda kwathu anthu ena kuyenera kutisonkhezera kulalikira.
3 Ntchito Yathu Yofunika Kwambiri: Timasonyeza kuti anthu limodzi ndi Yehova timawakonda ndi chikondi chenicheni mwa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuphunzitsa anthu choonadi cha Yehova ndi ntchito zake zodabwitsa. (Sal. 96:2, 3; 145:10-13) Komabe, mavuto atsiku ndi tsiku, nkhaŵa za moyo, ndi zinthu zocheukitsa zambirimbirizo zingatipatutse mosavuta pantchito yathu yolalikira. Motero tiyenera kumakumbukira kuti nthaŵi yochitira umboni choonadi cha Mulungu ndi Ufumu wake yatsala pang’ono kutha. Tisalole kupatutsidwa pantchito yofunika kwambiri imeneyi yopulumutsa moyo imene tapatsidwa kuti tichite. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kukhala otanganidwa mu utumiki wa Yehova kumatitetezera, ndipo kungabweretse mapindu osatha kwa amene akufuna kumva uthenga wa choonadi.—1 Akor. 15:58.
4 Kodi mungachite upainiya wothandiza kapena wokhazikika? Bwanji osalingalira mkhalidwe wanu ndi kuona ngati mungafutukule utumiki wanu mwa njirayi. Kodi munapuma pantchito? Bwanji osagwiritsa ntchito nthaŵi yanu mokwanira pa kulalikira? Achinyamata ambiri amene adakali pasukulu achita upainiya wothandiza mokhazikika. Iwo aupeza kukhala wotsitsimula mwauzimu ndi mwakuthupi, ndipo akhala ndi chimwemwe mumtima.
5 Kuti tikhoze kuchitira umboni choonadi mogwira mtima tifunika kukonza ndandanda ya nthaŵi yathu. (Aef. 5:15, 16) Mwezi watha, Sosaite inachepetsa maola ofunika kwa apainiya okhazikika kuchoka pa 90 kufika pa 70, ndipo kwa apainiya othandiza kuchoka pa 60 kufika pa 50. Choncho, upainiya wothandiza umafunika maola osakwana aŵiri patsiku pa mweziwo. Ena amasankha kudzuka ola limodzi nthaŵi yawo yoyambira kuchita zinthu isanakwane kuti apite mu utumiki asanapite ku sukulu kapena ku ntchito. Mukhozanso kulimbikitsidwa ndi kupeza malingaliro othandiza mwa kuyankhula ndi anthu ena amene achita bwino popanga ndandanda ya nthaŵi yawo yochitira upainiya wothandiza.
6 Nthaŵi zonse Yehova Mulungu wasonyeza ubwino kwa atumiki ake. Amene amutumikira mokhulupirika alandira madalitso ochuluka. Yehova akuchitirabe zabwino anthu amene amamukonda. Iye ndi wosangalala kulandira chilichonse chimene mikhalidwe yathu imatilola kuchita pamene tikuchitira umboni choonadi.—Aheb. 6:10.