Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/99 tsamba 8
  • Kuthandiza Ena Kuzindikira Phindu la Mabuku Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Ena Kuzindikira Phindu la Mabuku Athu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitira Umboni kwa “Anthu Onse”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Dzikonzereni Ulaliki Wanu wa Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Oyenerera ndi Okonzekera Kuphunzitsa Ena
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 1/99 tsamba 8

Kuthandiza Ena Kuzindikira Phindu la Mabuku Athu

1 “Mawu a Mulungu ngamoyo, ndipo amapereka mphamvu.” (Aheb. 4:12, NW) Popeza mabuku athu onena za m’Baibulo amathandiza anthu kupindula ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu, timawagwiritsa ntchito kusonkhezera chikondwerero m’Baibulo pamene tichitira umboni mwamwayi kapena popita kunyumba ndi nyumba.

2 Chinthu chotsimikizirika ndi chakuti, ngati mukudziŵa bwino zimene muti muyambe kuuza munthu musanamfikire ndi uthenga wa Ufumu, mudzakhala omasuka kwambiri ndiponso achidaliro kwambiri. Mawu anu adzasonyeza kuti mukufunadi kuuza ena uthenga wabwino. Kukonzekera kwanu bwino kumapangitsa utumiki wanu kukhala wosangalatsa kwambiri chifukwa mumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Chofunika kwambiri ndi chakuti timapanga nsembe yathu ya utumiki kukhala yabwino kwambiri imene tingapereke.—Aheb. 13:14; 1 Pet. 2:5.

3 Mabuku ogaŵira mu January ndi lililonse la masamba 192. Ngati muli nawo mabukuwa mu mpingo wanu, konzani ulaliki wanu wa uthenga wa Ufumu kotero kuti utsogolere ku mfundo yeniyeni m’buku limene mukugaŵira. Kodi mungachite motani zimenezo?

4 Mmene Mungakonzekerere: Choyamba, sankhani mawu m’buku limene mukugaŵira amene mwachionekere adzakondweretsa anthu oona mtima m’gawo lanu. Kenako, lingalirani chochitika chatsopano kapena nkhani ina imene ambiri angachite nayo chidwi imene mungakambirane ndi mwininyumba mwachidule musanamsonyeze mawu osindikizidwa amene mwasankha. Mwinamwake pali lemba losonyezedwa kapena logwidwa mawu limene mungaŵerenge, kaya m’Baibulo kapena mwachindunji kuchokera m’bukulo, kuti muchirikize mawu anuwo. Ngati munthuyo asangalatsidwa, mungamgaŵire bukulo. Mutatero kapena panthaŵi ina yabwino, fotokozani mwachidule mmene ntchito ya padziko lonse imeneyi imachirikizidwira ndi ndalama, ndipo gaŵirani bukulo pa chopereka cha nthaŵi zonse. Mulimonse mmene zingakhalire, yesani kumsiyira funso kapena nkhani imene mungagwiritse ntchito popanga ulendo wobwereza.

5 Mudzafupidwa chifukwa chothera nthaŵi ndi kuyesetsa kukonzekera ulaliki wanu wam’munda. Mungadalitsidwe mwa kuchita nawo mogwira mtima ntchito yosonkhanitsa imene ilikuchitika tsopanoli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena