Oyenerera ndi Okonzekera Kuphunzitsa Ena
1 Pamene Mose anaikidwa monga woimira Yehova, sanadzione kukhala woyenerera kulengeza mawu a Mulungu kwa Farao. (Eks. 4:10; 6:12) Yeremiya anavumbula kupanda chidaliro kwake mwa iye yekha cha kutumikira monga mneneri wa Yehova, nauza Mulungu kuti sanadziŵe kulankhula. (Yer. 1:6) Mosasamala kanthu za kupanda kwawo chidaliro poyamba, aneneri onse aŵiriwo anakhaladi mboni za Yehova zopanda mantha. Mulungu anawayeneretsa mokwanira.
2 Lerolino, chifukwa cha Yehova, tili nazo zonse zofunikira kuchitira utumiki wathu ndi chidaliro. (2 Akor. 3:4, 5; 2 Tim. 3:17) Mofanana ndi makanika wodziŵa bwino ntchito yake wokhala nazo zipangizo zokwanira, tili okonzekera bwino kuchita utumiki wathu mwaluso. M’January tidzagaŵira buku lililonse la masamba 192 limene linafalitsidwa isanafike 1984 limenenso mpingo ungakhale nalo. Ngakhale kuti zipangizo zauzimu zimenezi sizili zatsopano, mitu yake ya m’Malemba idakali yatsopano ndipo mabuku ameneŵa adzathandiza anthu kuphunzira choonadi. Mungagwiritsire ntchito maulaliki osonyezedwa panoŵa pa buku lililonse limene mukugaŵira.
3 Mungagwiritsire ntchito nkhani ya maphunziro kudzutsa chidwi pa Mawu a Mulungu. Mungayambitse makambitsirano mwa kunena kuti:
◼ “Maphunziro abwino ali ofunika kwambiri lerolino. Kodi muganiza kuti munthu ayenera kuchita maphunziro anji kuti apeze chimwemwe chachikulu ndi chipambano pa moyo wake? [Yembekezerani yankho.] Anthu amene amaphunzira za Mulungu ndiwo amene angapeze mapindu osatha. [Ŵerengani Miyambo 9:10, 11.] Buku ili [tchulani mutu wa buku limene mukugaŵira] lazikidwa pa Baibulo. Limasonyeza magwero okha a chidziŵitso chimene chingatsogolere ku moyo wosatha.” Sonyezani chitsanzo chimodzi m’bukulo. Ndiyeno ligaŵireni.
4 Pamene mubwerera kwa mwini nyumba amene munakambitsirana naye za kufunika kwa kuphunzira Baibulo, munganene kuti:
◼ “Ulendo watha tinakambitsirana kuti Baibulo limatipatsa maphunziro omwe angatitsogolere ku moyo wosatha. Koma pamafunikira khama kuti tiphunzire zimene tifunikira kudziŵa m’Malemba. [Ŵerengani Miyambo 2:1-5.] Anthu ambiri kumawavuta kumvetsetsa mbali zina za Baibulo. Lekani ndikusonyezeni mwachidule njira imene tagwiritsira ntchito kwambiri kuthandizira anthu kuti aphunzire zambiri pa ziphunzitso zoyambirira za Baibulo.” Mwa kugwiritsira ntchito buku limene mudalisiyalo, tsegulani pamalo oyenera ndipo sonyezani mwachidule kachitidwe ka phunziro la Baibulo. Ngati mwini nyumbayo akufuna kukhala ndi phunziro lokhazikika, fotokozani kuti mudzabweranso ndi buku lathu lophunziramo lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
5 Anthu ambiri akuvutika maganizo poona kuvutika kwa mamiliyoni a ana padziko. Mwinamwake mungathandize mwini nyumba kuona mmene Mulungu amaonera mkhalidwe umenewu, mwa kunena kuti:
◼ “Ndikhulupirira kuti mwaona malipoti a panyuzi onena za ana anjala, odwala, ndi onyalanyazidwa padziko. Kodi nchifukwa ninji mabungwe osamalira nkhani zimenezi sanakhoze kuwongolera mkhalidwewo? [Yembekezerani yankho.] Mulungu amafuna kuti anthu akhale ndi zabwino zokhazokha. Onani zimene iye akulonjeza ana ndi achikulire omwe, zolembedwa m’Baibulo. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:4.] Buku ili [tchulani mutu wake] limanena zambiri za dziko limene Mulungu akukonza limene simudzakhala kuvutika.” Ngati kuli kotheka, tsegulani pa chithunzi chosonyeza Paradaiso, ndi kukambitsirana chimenecho. Gaŵirani bukulo, ndipo panganani za ulendo wina.
6 Ngati poyamba munakambitsirana za ana ovutika, ulendo wotsatira mungapitirize nkhaniyo mwa kunena kuti:
◼ “Pamene ndinali pano posachedwapa, munasonyeza nkhaŵa yanu pa mkhalidwe wa ana omwe akuvutika chifukwa cha nyumba zimene zikupasuka, njala, matenda, ndi chiwawa. Kumatonthoza kuŵerenga m’Baibulo za dziko limene ana kapena achikulire sadzavutikanso ndi matenda, zoŵaŵitsa, kapena imfa. Ulosi m’buku la Yesaya umalongosola moyo wabwinopo umene udzadza padziko lapansi.” Ŵerengani ndi kukambitsirana Yesaya 65:20-25. Gwirizanitsani ndi phunziro la Baibulo lamtsogolo m’buku la Chidziŵitso.
7 Popeza kuti nkhani ya kupemphera ili yofala kwa anthu opembedza, mungayambitse makambitsirano pankhaniyi mwa kunena kuti:
◼ “Nthaŵi ina m’moyo wathu, ambiri a ife takumana ndi mavuto omwe atisonkhezera kupempherera thandizo kwa Mulungu. Komabe, ambiri amaona kuti mapemphero awo samayankhidwa. Zimaonekadi kuti ngakhale atsogoleri achipembedzo omwe amapempherera mtendere poyera mapemphero awo samamvedwa. Tikunena zimenezo chifukwa chakuti nkhondo ndi ziwawa zikupitiriza kuvutitsa mtundu wa munthu. Kodi Mulungu amamvetseradi mapemphero? Ngati amatero, nchifukwa ninji mapemphero ambiri amaoneka kuti sakuyankhidwa? [Yembekezerani yankho.] Salmo 145:18 limafotokoza chofunika kuti mapemphero athu ayankhidwe. [Ŵerengani lembalo.] Choyamba, mapemphero kwa Mulungu ayenera kukhala oona mtima ndi ogwirizana ndi choonadi cha m’Mawu ake, Baibulo.” Onetsani buku limene mukugaŵira, ndipo sonyezani zimene limanena pa phindu la kupemphera.
8 Pobwerera kumene munakambitsirana za pemphero, mungayese mafikidwe aŵa:
◼ “Ndinasangalala ndi makambitsirano athu aja pankhani ya pemphero. Ndikhulupirira malingaliro a Yesu pa zimene tiyenera kupempherera mudzawapeza kukhala chitsogozo chothandiza.” Ŵerengani Mateyu 6:9, 10, ndi kutchula zinthu zazikulu zimene Yesu anasonyeza m’pemphero lake lachitsanzo. Sonyezani mutu 16, “Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu,” m’buku la Chidziŵitso, ndipo funsani ngati mungasonyeze kaphunziridwe kake.
9 Ponena za kupatsa ena chidziŵitso cha Mulungu, tingafunse kuti, ‘Kodi woyenerera bwino ndani kuchita zinthu izi?’ Malemba amayankha kuti: ‘Ndife.’—2 Akor. 2:16, 17, NW.