Kuchitira Umboni kwa “Anthu Onse”
1 Tikamakumana ndi anthu a mikhalidwe kapena zipembedzo zosiyanasiyana, timakumbukira kuti chifuniro cha Yehova nchakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Kuwonjezera pa matrakiti ndi mabrosha okonzedwa mwapadera, tilinso ndi buku labwino kwambiri limene tingagwiritsire ntchito nthaŵi iliyonse kuthandiza anthu amene chipembedzo chawo sichinawaphunzitse choonadi ponena za Mulungu ndi Kristu.
2 Buku la Munthu Wamkulu limatithandiza kuwadziŵa onse aŵiri, Yesu ndi Mulungu. (Yoh. 14:9) Wachinyamata wina wazaka 12 ponena za bukulo anati: “Linanditonthoza kwambiri moti ndinapemphera kwa Yehova ndi misozi yachimwemwe nditangoliŵerenga kumene. Linandikhutiritsa mumtima mwanga kuti Yehova limodzi ndi Yesu akutiyang’anira.” Pa Yohane 17:3, Yesu anati, kuti tipeze moyo wosatha tiyenera kudziŵa Yehova ndi Mwana wake. Kuphunzira buku limeneli lonena za moyo wa Yesu kungatithandize kudziŵa bwino umunthu wa Yehova chifukwa Yesu ndiye “chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Aheb. 1:3) Panthaŵi iliyonse pamene kuli koyenera kuti mugaŵire buku limeneli, mungakonde kuyesa malingaliro otsatirawa.
3 Ngati mukuganiza kuti zingakhale bwino kumgaŵira wina buku la “Munthu Wamkulu,” mungafunse kuti:
◼ “Kodi mumakumbukiranji mukamaganiza za Yesu? [Yembekezerani yankho.] Olemba mbiri ochuluka amavomereza kuti Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. [Perekani chitsanzo cha m’mawu oyamba a buku la Munthu Wamkulu.] Baibulo limasonyeza kuti moyo wa Yesu unali chitsanzo choti ife titsanzire.” Ŵerengani 1 Petro 2:21 ndiyeno msonyezeni ndime yoyamba patsamba lotsirizira la mawu oyamba a m’buku la Munthu Wamkulu. Ngati mwini nyumbayo akufuna kuphunzira za Yesu, ligaŵireni bukulo. Musanachoke, ŵerengani Yohane 17:3 ndiye mfunseni kuti, “Kodi tingachipeze bwanji chidziŵitso chimenechi chotsogolera ku moyo wosatha?” Panganani kudzabwererako kuti mukayankhe.
4 Ngati mwabwerera kuti mukafotokoze mmene tingapezere chidziŵitso chopatsa moyo, munganene kuti:
◼ “Paja ndinalonjeza kuti ndidzabwera kudzakusonyezani mmene tingapezere chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha.” Sonyezani buku la Chidziŵitso, ndipo msonyezeni mmene timaphunzirira, mukumagwiritsira ntchito mutu woyamba.
5 Kapena mutamuuza dzina lanu, munganene mawu otsatirawa ngati anuanu:
◼ “Anthu ambiri adzifunsa kuti Yesu anali munthu wotani pamene anali kukhala padziko lapansi pano. Kodi mukuganiza kuti anasiyana ndi ena m’njira ziti? [Yembekezerani yankho.] Buku losangalatsali, lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, likusimba zinthu zazikulu m’moyo wa Yesu ndi zimene anachita mu utumiki wake, ndipo limathandiza kumvetsetsa kuti iye anali munthu wotani. Ena, ataliŵerenga, amaona ngati kuti apeza mpata wocheza naye, kuvutika limodzi naye, ngati kuti amuona ndi maso akuchita utumiki wake.” Msonyezeni chithunzi choyamba cha m’bukulo, chomwenso chili ndi mutu wabukulo. Ndiyeno pitani pamawu oyamba, ndipo ŵerengani ndime yachiŵiri pakamutu kakang’ono kakuti “Pindulani Mwa Kuphunzira za Iye.” Ngati walikonda, ligaŵireni.
6 Nali lingaliro lina:
◼ Achinyamata ambiri akufunafuna anthu oti aziwatsanzira, komano anthu abwinowo akusoŵa. Yesu Kristu anasiyira aliyense chitsanzo chabwino kopambana. [Ŵerengani 1 Petro 2:21.] Zochita zake zonse zinagwirizana ndi kulambira Atate wake wakumwamba. Nanga mukuganiza kuti zikanakhala bwanji ngati anthu onse anayesa kumtsanzira?” Yembekezerani ayankhe. Pitani pandime yachitatu patsamba lotsatana ndi tsamba lotsiriza m’bukumo, yomwe ikufotokoza mikhalidwe yake yapadera. Longosolani mmene buku la Munthu Wamkulu lingatithandizire tonsefe kukhala Akristu abwinopo. Ligaŵireni pachopereka chanthaŵi zonse. Zimenezo zingatheketse kuyamba phunziro mwina ndi brosha lakuti Mulungu Amafunanji kapena ndi buku la Chidziŵitso.
7 Mwinatu mungakonde kugwiritsira ntchito mawu ngati awa:
◼ “Munthu wina akangotchula Yesu Kristu, anthu ambiri amangoganiza za iye ali khanda kapena munthu wozunzidwa wongotsala pang’ono kufa. Zimene amangodziŵa basi ponena za Yesu ndizo kubadwa kwake ndi imfa yake. Zinthu zodabwitsa zimene ananena ndi kuchita pamoyo wake sizimatchulidwatchulidwa. Zimene iye anachita zimakhudza munthu aliyense amene anakhalapo padziko lapansi lino. Nchifukwa chake kuli kofunika kwambiri kuphunzira zinthu zambiri zosangalatsa zimene anatichitira.” Ŵerengani Yohane 17:3. Tsegulani patsamba loyamba la mawu oyamba a buku la Munthu Wamkulu, ndiyeno ŵerengani ndime yachinayi. Mfotokozereni mmene angalipezere bukulo nkumaliphunzira yekha.
8 Anthu osiyanasiyana oona mtima akufufuza choonadi ponena za Mulungu ndi Kristu. Tingawathandize pamene tili pantchito yathu yochitira umboni. Choncho, tiyenitu ‘tigwiritse ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse.’—1 Tim. 4:10.