Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/99 tsamba 1
  • “Lezani Mtima”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Lezani Mtima”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kuleza Mtima N’kofunika Kwambiri pa Utumiki Wathu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Pitirizani Kukhala Oleza Mtima
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova ndi Yesu
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Mungasonyeze Kuleza Mtima?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 1/99 tsamba 1

“Lezani Mtima”

1 Pamene tikuona kuti dongosolo lakale la Satana latsala pang’ono kwambiri kuti lithe, ‘kuleza mtima’ ndi kofunika kwambiri pamene tikuyembekezera tsiku la chilanditso la Yehova. Makamaka m’nthaŵi ya kumapeto ino, makamu a adani oipa ali ofunitsitsa kuchotsa malingaliro athu pankhani yofunika kwambiri ya uchifumu wa Yehova ndipo amatiyesa kuti ticheukitsidwe ndi zinthu zambirimbiri zotisangalatsa. Mwa njirayi, Satana angatichenjerere kuti tisiye kapena kuti tizigwira mwaulesi ntchito yolalikira Ufumu. (Yak. 5:7, 8; Mat. 24:13, 14) Kodi tingasonyeze kuleza mtima kofunikako m’njira zotani?

2 mwa Kukhala Wodziletsa: Pamene tikumana ndi anthu amphwayi kapena otsutsa mu utumiki wathu, kudziletsa kudzatithandiza kupirira polalikira. Sitidzaopsedwa kapena kukhumudwa mwamsanga ngati anthu amene tikumana nawo ali a mtima wasontho kapena opanda chifundo. (1 Pet. 2:23) Mphamvu yam’kati imeneyi ingatiteteze kuti tisamalankhule zoipa za anthu amene ali m’gawo lathu amene sagwirizana kapena kudana ndi ntchito yathu, tikumazindikira kuti nkhani zoterezo zikhoza kutifooketsa ifeyo ndi anthu amene timagwira nawo ntchito mu utumiki.

3 mwa Kupirira Moleza Mtima: Kuleza mtima kungakhale kovuta pamene munthu amene anasonyeza chidwi titacheza naye mu utumiki wakumunda sitikumpezanso panyumba. Zingakhalenso choncho ngati anthu amene tikuphunzira nawo akupita patsogolo pang’onopang’ono kapena akuchedwa kuima m’choonadi. Komabe, kupirira moleza mtima kaŵirikaŵiri kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. (Agal. 6:9) Mlongo wina anapanga maulendo obwereza angapo kwa mkazi wina asanayambitse phunziro la Baibulo. Pamaulendo oyambirira asanu, mkaziyo anali wotanganidwa ndi zinthu zina. Paulendo wachisanu ndi chimodzi, mlongoyo ananyowa ndi mvula yamabingu, komano nkusakapeza munthu aliyense panyumbapo. Komabe, pokhala wofunitsitsa kumpatsa ndithu mwayi mkaziyo, mlongoyo anafikanso ndipo anapeza kuti mkazi uja anali wokonzeka kuphunzira. Kuchokera pamenepo, wophunzirayo anapita patsogolo kwambiri ndipo m’kanthaŵi kochepa anapatulira moyo wake kwa Yehova.

4 Tikudziŵa kuti tsiku la Yehova silidzachedwa. Choncho tikuyembekezera mmene iye adzachitira zinthu, tikumadziŵa kuti kuleza mtima kwaumulungu kudzabala zipatso zabwino. (Hab. 2:3; 2 Pet. 3:9-15) Tiyenera kukhala oleza mtima monga mmene amakhalira Yehova ndi kusasiya utumiki. “Mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima,” yang’anani kwa Yehova kuti adzakupatseni mphotho kaamba ka kugwira kwanu ntchito zolimba.—Aheb. 6:10-12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena