Chimene Tasankha—Kulondola Njira ya Moyo ya Yehova
1 Mbali yaikulu ya Misonkhano Yachigawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” inali kuvomereza chosankha chimene chinali m’nkhani yomalizira. Chinayamba ndi chilengezo chakuti: “Ifeyo . . . tikuvomereza ndi mtima wonse kuti njira ya Mulungu ndiyo njira yabwino koposa ya moyo.” Kumbukirani mfundo zina zofunika kwambiri m’chosankha chimene chija zimene tinanena kuti, “TIKUVOMEREZA!”
2 Tinasankha kukhalabe oyera pamaso pa Yehova, osachitidwa maŵanga ndi dziko. Tidzapitiriza kuika chifuno cha Mulungu pamalo oyamba m’moyo wathu. Mwa kugwiritsa ntchito Mawu ake, Baibulo, ngati chotitsogoza chathu, sitidzatembenukira kulamanja kapena kulamanzere, motero tikumatsimikizira kuti njira ya Mulungu ndi yopambana njira ya dziko.
3 Kaŵirikaŵiri dziko limanyalanyaza njira ya moyo ya Mulungu ndipo limatuta zotsatirapo zake. (Yer. 10:23) Motero tiyenera kupitiriza kuphunzitsidwa ndi Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, amene amati: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.” (Yes. 30:21) Njira ya moyo ya Yehova, monga momwe Malemba akuilongosolera ndi yopambana m’njira iliyonse. Kuti tilondole njira imeneyo, ndi koyenera kugwiritsa ntchito mwayi wa chilichonse chimene Yehova amatiphunzitsa.
4 Pologalamu ya Maphunziro a Pamwamba ya Yehova: Yehova amatiphunzitsa chimene chili chifuno chenicheni cha moyo ndi mmene tingaugwiritsire ntchito kuti tipindule kwambiri. Amatiphunzitsa mmene tingawongolerere moyo wathu mwamaganizo, mwamakhalidwe ndi mwauzimu. Amatiphunzitsa mmene tingakhalire mwamtendere ndi abale athu, a m’banja lathu, ndinso anthu ena. Amachita zimenezi kupyolera m’buku lake lophunzitsira, Baibulo, ndiponso mwa gulu lake.
5 Misonkhano yathu yampingo ndi yofunika kwambiri pambaliyi. Pamene tifika mokhazikika ndi kutengamo mbali m’misonkhano yonse isanu, timalandira maphunziro ochuluka monga atumiki a uthenga wabwino ndipo timalandiranso maphunziro olinganizidwa bwino a moyo wachikristu. (2 Tim. 3:16, 17) Mlangizi wathu Wamkulu amatipatsanso maphunziro a teokalase mwa misonkhano yadera ndi yachigawo. Cholinga chathu chikhale kusaphonya msonkhano uliwonse kapena mbali yake iliyonse ngati thanzi ndi mikhalidwe yathu ikutilola kufikapo.
6 Tipitirizetu kulondola njira ya moyo ya Mulungu mwakhama m’masiku akudzawa, zonsezi kaamba ka chitamando cha Yehova ndi phindu lathu losatha!—Yes. 48:17.