Kusintha Maola Ofunika kwa Apainiya
1 Tonse timayamikira kukhala ndi apainiya okhazikika ndi othandiza amene amagwira ntchito zolimba m’mpingo. Ngakhale kumene gawo lili lochepa ndipo limafoledwa bwino kaŵirikaŵiri, apainiya apereka chitsanzo chabwino chifukwa cha changu chawo mu utumiki wa Ufumu. Alimbikitsa ofalitsa onse kuti akhale otanganidwa kufunafuna amene ali “ofuna.”—Mac. 13:48, NW.
2 Sosaite yaona mavuto opitirizabe amene apainiya amakumana nawo, makamaka pofuna kupeza ntchito yaganyu imene ingawatheketse kupeza zosoŵa zawo kotero kuti apitirizebe kukhala mu utumiki wa nthaŵi zonse. Mkhalidwe wa zachuma umene uli m’mayiko ambiri wapangitsanso kukhala kovuta kwambiri kwa anthu ena kuti ayambe ntchito yaupainiya, ngakhale kuti chimenechi ndi chikhumbo chawo chachikulu. M’miyezi yapitayi, zifukwa zimenezi ndi zinanso zalingaliridwa mosamalitsa.
3 Motero, polingalira zimene tanenazo, Sosaite yachepetsa maola ofunika kwa onse, apainiya okhazikika ndi othandiza omwe. Kuyambira chaka cha 1999, maola amene adzafunika kwa apainiya okhazikika ndi 70 mwezi uliwonse, kapena kuti 840 onse pamodzi pachaka. Apainiya othandiza adzafunika maola 50 pamwezi. Maola ofunika kwa apainiya apadera ndi amishonale sanasinthe, chifukwa Sosaite imawathandiza kusamalira zosoŵa zawo zakuthupi zikuluzikulu. Motero iwo angaike malingaliro awo onse pa ntchito yawo yolalikira ndi kupanga ophunzira.
4 Tikukhulupirira kuti kusintha maola ofunika kumeneku kudzathandiza apainiya ambiri kusasiya utumiki wamtengo wapataliwu. Zikuyeneranso kulimbikitsa ofalitsa ochuluka kuyamba ntchito yaupainiya wokhazikika ndi wothandiza. Zimenezi zikhaletu dalitso lalikulu kwa aliyense m’mpingo!