Lilemekezeni Kwambiri Dzina Lokoma la Yehova
1 Pamene Satana anachimwitsa makolo athu oyambirira, iye anaipitsa dzina la Mulungu. Mdyerekezi ananena kuti Yehova anamunamiza Adamu. (Gen. 3:1-5) Popeza kuti dzina la Mulungu n’logwirizana ndi mphamvu yake yokwaniritsa mawu ake, zonena za Satana zinali zaugogodi. Mwa kukwaniritsa pang’onopang’ono zolinga zake zaumulungu, Yehova wachotsa chitonzo pa dzina lake n’kulikhalitsa lokoma.—Yes. 63:12-14.
2 Ndife anthu amene Yehova ‘watitcha ndi dzina lake.’ (Mac. 15:14, 17) Izi zimatipatsa ife mwayi wosonyeza mmene timaonera za kuyeretsedwa kwake. Timaona dzina la Yehova kukhala lokoma kwambiri, popeza limaimira zinthu zonse zabwino, zokoma mtima, zachikondi, zachifundo, ndi zolungama. Timachita mantha ndi ukulu wa dzina laulemerero la Mulungu. (Sal. 8:1; 99:3; 148:13) Kodi tiyenera kulimbikitsidwa kuchitanji?
3 Yeretsani Dzina la Mulungu: Dzina la Mulungu silingayeretsedwe kuposa mmene lili. Koma mwa makhalidwe athu oyera ndi mwa kulalikira za Ufumu, tingasonyeze kuti timaona dzina la Mulungu kukhala lolemekezeka kwambiri. Tiyeni tifuule kuti: “Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa [“likwezedwe,” NW].” (Yes. 12:4) Kodi zimenezi tingazichite motani?
4 Tingapezerepo mwayi pampata uliwonse kulengeza dzina la Yehova ndi zonse zimene limaimira. Ntchito yathu yolalikira imalemekeza Yehova, kaya ndi yokonzekera kapena yamwamwayi, yakunyumba ndi nyumba kapena ya kusitolo ndi sitolo, yapamsewu kapena yapatelefoni. Pamene tapeza anthu achidwi amene akumvetsera, tiyenera kupanga makonzedwe enieni akuti tidzawafikirenso ndi kuwaphunzitsa zambiri ponena za Yehova. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kukwaniritsa zimene tapanganazo komanso kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ubwino wake n’ngwakuti chaka chilichonse anthu zikwi mazana ambiri amafika pakulidziŵa dzina lokoma la Yehova, kulilemekeza, ndi kuliyeretsa.
5 Kuchita nawo kwathu ntchito yolemekeza dzina la Mulungu ndi mtima wonse kumasonyeza bwino mbali imene ife tili pankhani imene Satana anadzutsa mu Edene. Iyi ndiyo ntchito yabwino, yolemekezeka kwambiri imene tingaigwire. Tiyeni tililemekeze ndi kulitamanda dzina lokoma la Yehova mwachangu!—1 Mbiri 29:13.