Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/99 tsamba 2-7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 9/99 tsamba 2-7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mutapeza ochita chidwi pa maulendo obwereza, mungagaŵire masabusikiripishoni. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

◼ Tazindikira kuti ofalitsa ena amene akugwirizana ndi mipingo sadzidziŵikitsa kwa Mboni zinzawo zimene zimagaŵira magazini ndi zofalitsa zina m’khwalala. Ndiyeno “amagula” magazini ndi zofalitsa zambiri kwa Mboni zinzawo zija popanda kudzidziŵikitsa kuti iwonso ndi Mboni. Izi sizoyenera chifukwa amapangitsa kuti magaziniwo achitiridwe lipoti kaŵiri, zikumachititsa mpingo kukhala ndi lipoti labodza pa chiŵerengero cha zofalitsa zimene zafalitsidwa m’gawo kwa anthu okondwerera. Zimaperekanso chikondwerero chonama kwa Mboni inzathu imene ingamaganize kuti yagaŵira zofalitsa zambiri kwa anthu okondwerera, osadziŵa kuti zofalitsa zimenezo zapitanso m’zikwama za Mboni zina. Choncho, tikupempha ofalitsa onse kuti azidzidziŵikitsa monga Mboni za Yehova mwamsanga Mboni ikawafikira.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamusankha ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Akatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mutapereka lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za wochotsedwa aliyense kapena munthu wodzilekanitsa amene angakonde kubwezeretsedwa.

◼ Amene akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikiripishoni onse atsopano komanso olembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikiripishoni awo, kupyolera mu mpingo.

◼ Sosaite silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akufuna. Woyang’anira wotsogoza azikonza chilengezo mwezi uliwonse isanatumizidwe oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo ku Sosaite kuti onse amene akufuna mabuku angauze mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.

◼ Misonkhano Yachigawo ndi ya Mitundu Yonse ya 1998 ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” inalidi dalitso kwa onse opezekapo. Mwa opezekapo anali amishonale 2,764 ndi atumiki a padziko lonse amene anatha kupita ku mayiko akwawo mothandizidwa ndi zopereka zodzifunira za mipingo. Tikuyamikira kuchirikiza kwanu makonzedwe ameneŵa. Poti misonkhano imeneyi yatha, ndalama zotsala zigwiritsidwa ntchito kuchirikiza ntchito yolalikira yapadziko lonse.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

1998 Watchtower Publications Index—Chingelezi

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chifulenchi

Apply Yourself to Reading and Writing (Chida chatsopano chothandiza kuphunzira kuŵerenga)—Chingelezi

◼ Kuyamba ndi kope la September 1, 1999, Nsanja ya Olonda idzakhalako m’Chikazakhi ndipo izituluka kamodzi pamwezi.

Zapitirizidwa patsamba 7

Zilengezo (kuchokera patsamba 2)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena