Misonkhano ya Utumiki ya September
Mlungu Woyambira September 6
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 17: “Kodi Mukugwira Ntchito ndi Cholinga?” Kambani mawu oyamba kwa mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu buku la Uminisitala Wathu, masamba 88-9. Limbikitsani onse kukhala akhama komanso kuchita zonse zotheka mu utumiki wawo.
Mph. 18: “Makolo—Onetsani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu.” Mkulu apereke mawu oyamba mwachidule, kenako abale aŵiri amene ali makolo akambirane. Ali ndi nkhaŵa ya mmene angatetezere ana awo ku zinthu zoipa zimene amaona kusukulu, pawailesi yakanema, ndi kwa achibale awo amene sali Mboni ndi ena. Abalewo apende makhalidwe oipa, malankhulidwe ndi mapesedwe achikunja, ndi zosangalatsa zoipa. Akatha kunena kufunika koonetsa chitsanzo chabwino, akambirane njira zokulitsira changu cha phunziro la banja, misonkhano ya mpingo, ndi utumiki wakumunda.—Onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, masamba 8-22.
Nyimbo Na. 101 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Kodi Tinachita Motani Chaka Chatha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Afotokoze mbali zazikulu kuchokera pa lipoti la mpingo la chaka chautumiki cha 1999. Yamikirani zinthu zabwino zimene zinachitika. Tchulani mbali zimene zikufunika kuwongolera. Fotokozani mmene mpingo wachitira pa chiŵerengero cha opezeka pamisonkhano ndi pochititsa maphunziro a Baibulo. Nenani zolinga zanu zotheka za chaka chimene chayambacho.
Mph. 20: “Kodi Mukanena Chiyani kwa Mhindu?” Mafunso ndi mayankho. Gogomezani ubwino wokamba zimene munthu angagwirizane nazo ndipo nenani zimene tingagwirizanepo ndi Mhindu. Sonyezani mmene zitsanzo za ulaliki zingasinthidwire kuti tilalikire anthu achipembedzo china chilichonse. Onetsani chitsanzo cha ulaliki wokonzedwa bwino wolalikira kwa Mhindu. Nkhani zina za Chihindu mungazipeze m’buku la Kukambitsirana, tsamba 22.
Nyimbo Na. 140 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 20
Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zokumana nazo za mu utumiki wakumunda.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Kodi Tikupanga Ophunzira? Woyang’anira utumiki akambirane ndi mtumiki wotumikira mmodzi kapena aŵiri mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1996, masamba 19-22. Gogomezerani kuchokera m’Malemba zifukwa zake tiyenera kufunafuna oyenera m’gawo lathu ndi kuwapanga kukhala ophunzira. (Mat. 10:11) Ameneŵa ndi amene akulira chifukwa cha kuipa ndi mikhalidwe yonyansa imene amaiona ndipo ndi amene amafuna Yehova tsiku lake la mkwiyo lisanafike. (Ezek. 9:4; Zef. 2:2, 3) Pakati pawo pali awo “ofuna moyo wosatha.” (Mac. 13:48, NW) Ntchito yathu ndi kupanga ophunzira, kuphunzitsa anthu onse zinthu zimene Yesu analamula. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Pamene kuli kwakuti ntchito ya kunyumba ndi nyumba, ndi umboni wamwamwayi, ndi ntchito ya m’khwalala ingathe kudzutsa chidwi mwa amene timakumana nawo, kupanga ophunzira kumachitika pamene tibwererako—pamaulendo obwereza ndi pamaphunziro a Baibulo. Nenani malingaliro othandiza a mmene zimenezi zingachitikire.
Nyimbo Na. 175 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 27
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a September a utumiki wakumunda. Limbikitsani onse kupanga makonzedwe odzagaŵira nawo magazini mokwanira mu October. Pendani malingaliro ena opezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1996, tsamba 8, a mmene tingakonzekerere ulaliki. Mwa kugwiritsa ntchito magazini atsopano, tchulani mfundo zabwino zoyenera kukambirana ndipo khalani ndi chitsanzo cha ulaliki wachidule umodzi kapena aŵiri.
Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 15: “Kulambira Koona Kukufutukuka Kummaŵa kwa Ulaya.” Mkulu achititse mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani zokumana nazo kapena umboni wa kuwonjezereka m’mayiko otchulidwawo, monga mmene ananenera ma Yearbook aposachedwapa.
Nyimbo Na. 87 ndi pemphero lomaliza.