Kodi Mukugwira Ntchito ndi Cholinga?
1 Yehova ndi Mulungu wa cholinga. (Yes. 55:10, 11) Timalimbikitsidwa kum’tsanzira. (Aef. 5:1) Izi ziyenera kusonyezedwa m’njira imene timachitira utumiki wathu. Chotero funsoli n’loyenera: “Kodi mukugwira ntchito ndi cholinga?”
2 Kulalikira kwanu kukhomo ndi khomo, kuchita umboni wamwamwayi, ndi kugaŵira mabuku, zonsezi ndi mbali za utumiki wokhala ndi cholinga. Koma dziŵani kuti ntchito yathu sindiyo kulalikira kokha komanso kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Tikatha kufesa mbewu za choonadi cha Ufumu, tiyenera kubwererako kukazithirira ndi kuzisamalira nthaŵi zonse, tikumayang’ana kwa Yehova kuti akulitse. (1 Akor. 3:6) Tiyenera kukhala akhama popanga maulendo obwereza ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
3 Wonjezerani Utumiki Wanu: Nthaŵi zonse zimasangalatsa ukaganiza zakale ndi kuona zimene unachita mu utumiki, ndipo chamumtima umati: “Ndinakwanitsa cholinga changa.” Monga momwe zalembedwera pa 2 Timoteo 4:5, Paulo analimbikitsa kuti: “Kwaniritsa utumiki wako.” Zimenezo zimaphatikizapo kuwonjezera zoyesayesa zanu zobwerera kwa onse amene anaonetsa chidwi. Pandandanda yanu ya utumiki ya mlungu uliwonse, konzani nthaŵi yotsimikizirika yopanga maulendo obwereza. Gwirani ntchito ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu ofuna chilungamo. Ichi chiyenera kukhala cholinga chanu pochita utumiki.
4 Funsani ofalitsa akuuzeni mmene anamvera kuona ophunzira Baibulo awo akubatizidwa pamsonkhano. Anasangalala, mwinanso mofanana ndi omwe ankabatizidwawo. Anakwaniritsadi cholinga chachikulu! Wopanga ophunzira wina anafotokoza motere: “Kupanga ophunzira ndiko kuwonjezera atamandi a Yehova. Ndi moyo kwa onse amene amalandira choonadi. Ndimakonda kuphunzitsa ena choonadi ndipo n’zosangalatsa kwambiri! . . . Ambiri amene afika pa kukonda Yehova akhala mabwenzi anga apamtima.”
5 Tangolingalirani kukhala wokhoza kuthandiza munthu wina kukhala mtumiki wa Yehova wodzipatulira! Si chimwemwe chake! Chipatso chimenechi chimadza chifukwa chogwira ntchito mu utumiki ndi cholinga.—Akol. 4:17.