Makolo—Onetsani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
1 Mawu a Mulungu amatiuza kuti “atate [ndi amayi] wa wolungama adzasekeradi.” (Miy. 23:24, 25) Ndi dalitso lalikulu kwa makolo amene akuonetsa chitsanzo chabwino kwa ana awo! Wa m’Komiti ya Nthambi wina anati ponena za makolo ake: “Moyo wawo wonse unali pachoonadi, ndipo ndinafuna kuti moyo wanganso ukhale pachoonadi.” Kodi ana ayenera kuona chiyani mwa makolo awo?
2 Makhalidwe Abwino ndi Ulemu: Ndi udindo wa makolo kukhomereza mikhalidwe yabwino mwa ana awo. Makhalidwe abwino amachita kuwaphunzira, osati mwa malangizo apakamwa okha, komanso mwa kuonera ndi kutsanzira. Choncho, kodi mumaonetsa makhalidwe otani? Kodi ana anu amakumvani mukunena kuti “pepani,” “chonde,” komanso “zikomo”? M’banja, kodi mumapatsana ulemu? Kodi mumamvetsera ena akamalankhula? Kodi mumamvetsera ana anu akamalankhula nanu? Kodi mikhalidwe yabwinoyi mumaionetsa ku Nyumba ya Ufumu ndi kunyumba kwanu?
3 Kulimba Mwauzimu ndi Kugwira Ntchito Mwachangu: Mbale amene wakhala zaka zoposa 50 mu utumiki wa nthaŵi zonse akukumbukira kuti: “Amayi ndi abambo anga anali chitsanzo chabwino kwambiri poyamikira misonkhano ndi pa changu mu utumiki.” Kodi mumasonyeza motani kwa ana anu kuti mumafunitsitsa kulimbitsa mkhalidwe wauzimu wa a m’nyumba mwanu? Kodi mumachitira pamodzi lemba la tsiku? Kodi mumakhala ndi phunziro la banja nthaŵi zonse? Kodi ana anu amakuonani mukuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa za Sosaite? Kodi amamva zotani mukamapemphera ndi banja? Kodi mumakambirana ndi ana anu zinthu zomangirira zauzimu, zinthu zabwino za choonadi komanso za mpingo? Kodi mumakonda kupezeka pamisonkhano yonse ndi kuchita utumiki wakumunda monga banja?
4 Makolo, onani chitsanzo chimene mukuonetsa kwa ana anu. Chikhale chabwino kwambiri, ndipo adzachiyamikira kwa moyo wawo wonse. Mkazi wa woyang’anira woyendayenda, amene tsopano ali ndi zaka za m’ma 70, anati: “Ndidakapindulabe ndi chitsanzo chabwino cha makolo anga achikondi achikristu. Ndipo ndi pemphero langa lapansi pa mtima kuti ndionetse kuyamikira kwanga konse choloŵa chimenechi mwa kuchigwiritsa ntchito bwino zaka zonse zilinkudza.”