Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/99 tsamba 3-6
  • Kulambira Koona Kukufutukuka Kummaŵa kwa Ulaya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulambira Koona Kukufutukuka Kummaŵa kwa Ulaya
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Ikuyenda Bwino
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Mmene Anthu Akuwonjezekera Pakufunika Nyumba Zina Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse M’mayiko Ena a ku Ulaya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 9/99 tsamba 3-6

Kulambira Koona Kukufutukuka Kummaŵa kwa Ulaya

1 Akristu a m’zaka za zana loyamba anali achangu polalikira Ufumu. Anakondwera pamene mipingo ‘inachuluka m’chiŵerengero chawo tsiku ndi tsiku.’ (Mac. 16:5) Kulalikira kwawo molimba mtima kunafikitsa kulambira koona ku Asia, Afirika, ndi ku Ulaya, ndipo kunachititsa kuti apeze okhulupirira ambiri.

2 M’nthaŵi ya mapeto ino, kulambira koona kukupitirira kufutukuka makamaka m’mayiko a Kummaŵa kwa Ulaya. Mayiko amene tinali oletsedwa ndi boma mpaka kumayambiriro a m’ma 1990, tsopano tikuwonjezeka kwambiri. Kope la 1999 Yearbook likusonyeza kuti mayiko aŵiri mwa ameneŵa, Russia ndi Ukraine, lililonse palokha linapereka lipoti la ofalitsa oposa 100,000 amene akuchita nawo utumiki wapoyera. Kuyambira 1991 magawo 15 m’dziko limene kale linkatchedwa Soviet Union anthu oposa 220,000 adzipatulira kwa Yehova ndipo abatizidwa! Kuwonjezereka kwakukulu kumeneku kwapangitsa kukhala kofunika kumanga Nyumba za Ufumu ndi za Msonkhano zatsopano zambiri komanso kuwonjezera chiŵerengero cha nthambi.

3 Monga momwe tinalengezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1997, tsopano ndalama zina za m’Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu zikugwiritsidwa ntchito kupereka ngongole ku mipingo ya m’mayiko amene kukufunika Nyumba za Ufumu zambiri koma kumene kuli mavuto aakulu a zipangizo zomangira ndi ndalama. Kuyambira March 1996 mpaka October 1998, Sosaite inavomereza mapempho 359 ochokera ku maofesi a nthambi oyang’anira mayiko 11 a Kummaŵa kwa Ulaya a ngongole zomangira Nyumba za Ufumu. Ndalama zoperekedwa zikugwiritsidwa ntchito kugulira malo ndi zipangizo zomangira Nyumba za Ufumu zatsopano ndiponso kuthandiza mipingo kukonzetsa nyumba zimene zilipo kale. Zithunzi zili panozi zikutisonyeza mmene ndalama zoperekedwa ku Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu ku United States ndi m’mayiko ena zapindulira abale athu Kummaŵa kwa Ulaya.

4 Mu 1998, dziko la Bulgaria linali ndi chiwonjezeko cha 12 peresenti, ndipo abale anali osangalala pamene Nyumba yawo ya Ufumu yoyamba anaipatulira m’April chaka chomwecho. Croatia anali ndi chiwonjezeko cha 4 peresenti, ndipo pakalipano abale akumanga Nyumba za Ufumu zowonjezereka ndi cholinga chopititsa patsogolo kulambira koona. Ku Hungary Nyumba za Ufumu ngati 80 zikugwiritsidwa ntchito ndi mipingo 144. Izi zikutanthauza kuti mwa mipingo 235 m’dziko limenelo, 61 peresenti ili ndi malo awo olambirira. Ku Macedonia pologalamu yomanga Nyumba za Ufumu yamaliza kumanga maholo atsopano aŵiri, ndipo enanso akumangidwa. Chilimwe cha 1999, nyumba imodzi yokhala ndi Nyumba za Ufumu ziŵiri inatsirizidwa kumangidwa ku likulu la Skopje. Holo imeneyi n’njaikulu moti itha kukwanira mipingo yosachepera isanu ndi umodzi.

5 Chaka chatha ku Russia, pa avareji, anthu oposa 260 ankabatizidwa mlungu uliwonse! Potengera chitsanzo cha mayiko ena, nthambi ya Russia tsopano yakhazikitsa Makomiti a Zigawo Omanga okwanira 12 m’gawo lawo lalikulu lonselo, kuti achirikize ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’tsogolo. Kumpoto kwa St. Petersburg, ntchito yomanga ili mkati kumanga Nyumba yoyamba ya Msonkhano m’dzikomo, imene idzakhale yokwanira anthu pafupifupi 1,600. Nyumbayi idzakhalanso ndi Nyumba za Ufumu zisanu iliyonse yokwana anthu 200. Pothandiza zosoŵa zauzimu za abale athu komanso za anthu ambiri okondwerera ku Ukraine, Nyumba za Ufumu 84 zatsirizidwa kumangidwa ndipo zina 80 zili mkati kumangidwa.

6 Kodi kuwonjezeka kumeneku Kummaŵa kwa Ulaya sikukudzetsa chimwemwe m’mitima yathu? Mosasamala kanthu za kumene timakhala, kufutukuka kwa kulambira koona kumatikumbutsa kuti Mulungu alibe tsankho ndi kuti kuleza mtima kwake kudzapangitsa “khamu lalikulu” kupulumuka. (Chiv. 7:9; 2 Pet. 3:9) Ndi mwayi wathu kuchirikiza nawo kukula kwauzimu kwa anthu ena, ngakhale a m’mayiko akutali! Miyambo 28:27 amatitsimikizira kuti “wogaŵira aumphaŵi sadzasoŵa.” Kufunitsitsa kwathu kuthandiza kulipirira ndalama zomangitsira zimenezi kukupangitsa “kulingana” kwa zinthu zakuthupi, ndipo kukutheketsa onse kupeza chimwemwe chimene chimadza n’kupatsa komanso chikondwerero chimene chimakhalapo poona kulambira koona kukufutukuka padziko lonse lapansi.—2 Akor. 8:14, 15; Mac. 20:35.

[Chithunzi patsamba 3]

Săcele, Romania

[Chithunzi patsamba 3]

Maardu, Estonia

[Chithunzi patsamba 3]

Sevnica, Slovenia

[Chithunzi patsamba 3]

Tiszavasvári, Hungary

[Chithunzi patsamba 4]

Jūrmala, Latvia

[Chithunzi patsamba 4]

Taurage, Lithuania

[Chithunzi patsamba 4]

Tallinn, Estonia

[Chithunzi patsamba 5]

Prievidza, Slovakia

[Chithunzi patsamba 5]

Mátészalka, Hungary

[Chithunzi patsamba 5]

Belgrade, Yugoslavia

[Chithunzi patsamba 6]

Ruma, Yugoslavia

[Chithunzi patsamba 6]

Vranov nad Topl’ou, Slovakia

[Chithunzi patsamba 6]

Tornakalns, Latvia

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena