Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/00 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira June 12
  • Mlungu Woyambira June 19
  • Mlungu Woyambira June 26
  • Mlungu Woyambira July 3
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 6/00 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira June 12

Nyimbo Na. 136

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 15: “Kuchititsa Kwanu Sikuli Chabe.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga pa chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1996, patsamba 32.

Mph. 22: Kuyambitsa Maphunziro ndi Bulosha la Mulungu Amafunanji. Nkhani. Pendani nkhani ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 1999, patsamba 6. Chitani chitsanzo chaulaliki umene uli m’ndime 6. Khalani ndi wofalitsa m’modzi kapena aŵiri asimbe mwachidule mmene apambanira poyambitsa maphunziro, anene mmene anayambira phunziro ndi zimene achita kuti azitha kuchititsa phunzirolo mlungu uliwonse.

Nyimbo Na. 209 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 19

Nyimbo Na. 14

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Ngati mpingo uli ndi mabuku a Achichepere Akufunsa kapena Youth, chitani chitsanzo cha mmene mabukuŵa angagwiritsidwire ntchito mogwira mtima muutumiki m’miyezi ikubwerayi, pamene timapeza achinyamata ambiri panyumba.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.

Mph. 20: “Musaiŵale Cholinga cha Ufulu Umene Mulungu Wakupatsani!” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 1-8 zankhaniyi. Ŵerengani ndime zonse ngati nthaŵi ilola, malemba operekedwawo angaŵerengedwe ndi kugogomezeredwa. Ikambidwe ndi mkulu woyeneretsedwa.

Nyimbo Na. 89 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 26

Nyimbo Na. 39

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a June. Pendani mabuku ogaŵira mu July. Onetsani mabulosha akale amene alipo pampingopo, ndipo nenani mwachidule cholinga cha bulosha lililonse. Chitani chitsanzo chokonzedwa bwino chosonyeza mmene tingagaŵire limodzi la mabulosha ameneŵa muutumiki.

Mph. 15: “Khalani Owoloŵa Manja, Okonzeka Kugaŵira Ena.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo zifukwa zinayi ‘Zimene Timapatsira’ zomwe zili mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1996, masamba 29-30.

Mph. 20: “Musaiŵale Cholinga cha Ufulu Umene Mulungu Wakupatsani!” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 9-16 zankhaniyi. Gwiritsani ntchito ndime 7 ndi 8 m’mawu anu oyamba m’mphindi imodzi. Ŵerengani ndime zonse ngati nthaŵi ilola, malemba operekedwawo angaŵerengedwe ndi kugogomezeredwa. Ikambidwe ndi mkulu woyeneretsedwa.

Nyimbo Na. 44 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 3

Nyimbo Na. 213

Mph. 5: Zilengezo za pampingo ndiponso zokumana nazo za muutumiki. Funsani ofalitsa amene anayambitsa maphunziro ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kuti afotokoze mmene anachitira.

Mph. 15: “Musaiŵale Cholinga cha Ufulu Umene Mulungu Wakupatsani!” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 17-23 zankhaniyi. Gwiritsani ntchito ndime 15 ndi 16 m’mawu anu oyamba m’mphindi imodzi. Ŵerengani ndime zonse ngati nthaŵi ilola, malemba operekedwawo angaŵerengedwe ndi kugogomezeredwa. Malizani nkhaniyi ndi bokosi lachidule cha nkhaniyi. Ikambidwe ndi mkulu woyeneretsedwa.

Mph. 25: “Ndingathe Bwanji, Popanda Munthu Wonditsogolera?” Yokambidwa ndi woyang’anira utumiki, kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani mokweza ndime iliyonse, ndipo ŵerengani malemba amene ali mu ndime 3, 4, ndi 7. Pokambirana ndime 6, fotokozani ntchito ya woyang’anira utumiki yoona ngati kuli koyenera kuti maphunziro a Baibulo ayenera kuyambidwanso ndi anthu obatizidwa kale.—Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 1998.

Nyimbo Na. 51 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena