Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira August 12
Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Fotokozani mwachidule mfundo za m’nkhani yakuti “Ŵerengani ndi Ana Anu,” kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1999, patsamba 25.
Mph. 20: “Khalani ndi Zolinga Zauzimu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 5, phatikizanipo mawu olimbikitsa pankhani ya upainiya wokhazikika ndi utumiki wa pa Beteli kuchokera mu buku la Utumiki Wathu, patsamba 114 mpaka 116.
Mph. 12: Zokumana nazo. Pemphani anthu mumpingomo kusimba zimene anakumana nazo pamene anali kugaŵira thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Kodi alipo ayambitsa maphunziro a Baibulo? Ngati alipo, afotokoze momwe anachitira kapena asonyeze chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za zomwe zinachitikazo. Pendani bokosi lakuti “Pofunika Kugaŵira Mathirakiti,” la mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2001, patsamba 4.
Nyimbo Na. 123 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 19
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani nkhani yakuti “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ukubwerawo, ndipo limbikitsani onse kukafika mofulumira ndiponso kukamvetsera mwatcheru pulogalamu yonse. Limbikitsani ofalitsa kuti aitanire anthu amene achita chidwi kumene ndiponso amene amaphunzira nawo Baibulo ku msonkhanowu.
Mph. 15: N’chifukwa Chiyani Amakana Kukambirana Nafe? Kukambirana ndi omvetsera komanso chitsanzo. Nthaŵi zambiri mu utumiki timakumana ndi anthu amene safuna kukambirana nawo zimene amakhulupirira. Izi zingatilepheretse kukambirana nawo uthenga wa Ufumu. Kudziŵa chifukwa chake munthu akukana kukambirana naye, kungatithandize kukonzekera ulaliki umene ungamulimbikitse kunena maganizo ake. Kambiranani momwe tingachitire ulaliki wathu ngati takumana ndi anthu ngati awa: (1) Amene alibe chidwi ndi chipembedzo, ngakhale chawo chomwe. (2) Amene amakonda kwambiri miyambo ya chipembedzo cha banja lawo ndi cha makolo awo. (3) Amene samasuka kufotokoza zimene amakhulupirira chifukwa alibe nazo umboni wokwanira wa m’Malemba. (4) Amene amatida chifukwa cha zinthu zabodza zimene otsutsa amanena. Sinthani zinthu tatchulazi ngati n’kofunika kuti zigwirizane ndi gawo la mpingowo, makamaka ndi zimene mumakumana nazo kwambiri m’deralo. Phatikizanipo chitsanzo chachidule cha ulaliki chosonyeza zomwe tingachite kuti tilimbikitse munthu kukambirana naye za m’Malemba.
Mph. 18: “Khalani Wokhulupirika ku Chikristu Wachibale Akachotsedwa mu Mpingo.” (Ndime 1-8) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi. Ikambidwe ndi mkulu woyeneretsedwa bwino, agwiritse ntchito mafunso amene ali m’nkhaniyi. Mbale amene amaŵerenga bwino aŵerenge ndime iliyonse mokweza.
Nyimbo Na. 136 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 26
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za ulaliki za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya August 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye, akuti “Kodi n’chifukwa ninji anthu inu mumafika mwakaŵirikaŵiri?”—Onani buku la Kukambitsirana, patsamba 20.
Mph. 15: “Lankhulanani!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 18: “Khalani Wokhulupirika ku Chikristu Wachibale Akachotsedwa mu Mpingo.” (Ndime 9-14) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi. Ikambidwe ndi mkulu woyeneretsedwa bwino, gwiritsani ntchito mafunso ali m’nkhaniyi. Mbale amene amaŵerenga bwino aŵerenge ndime iliyonse mokweza.
Nyimbo Na. 125 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 2
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a August. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, mpainiya wokhazikika kapena wothandiza achite chitsanzo cha momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya September 1, ndipo wofalitsa wa mpingo asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya August 8. Limbikitsani ofalitsa onse kuŵerenga lemba mu ulaliki wawo.
Mph. 20: Konzekerani Musanapite. Kukambirana ndiponso chitsanzo. Kukonzekera bwino kumathandiza kuti zinthu zitiyendere bwino mu utumiki. Choncho nthaŵi idakalipo, (1) Pezani zofalitsa zimene mukagwiritse ntchito. (2) Onetsetsani kuti muli ndi mapepala olembapo za kunyumba ndi nyumba ndi bolopeni kapena pensulo. (3) Ngati mukuona kuti mudzafunika zoyendera, konzani dongosolo loyenera la kayendedwe. (4) Ganizirani za maulendo obwereza amene mwakonza kuchita. (5) Konzekerani zimene mukanene. Ngati mukachititsa msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda, pezani gawo lokwanira. Kambiranani ndi omvetsera njira ziŵiri kapena zitatu za momwe tingachitire pogaŵira buku la Chidziŵitso mu utumiki mu September. Sonyezani chitsanzo cha njira imodzi mwa njira zimenezi, ndipo phatikizanipo lemba m’makambiranowo.—Onani mfundo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1996, tsamba 8, ndi wa June 1995, tsamba 8.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo. Kapena pemphani anthu mumpingomo kusimba zimene anakumana nazo polalikira mwamwayi, mwina pouza uthenga wabwino anthu kumalo oimikako galimoto, m’zoyendera za anthu onse, ku msika, ku masitolo, koima malole onyamula katundu ndi m’malo ena. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri cha zomwe zinachitikazo.
Nyimbo Na. 99 ndi pemphero lomaliza.