Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 9
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo. Popenda ndime 2, sonyezani ndandanda yophunzirira. Popenda ndime 3, ŵerengani ndi kukambirana ndime 23 patsamba 25 m’bukulo.
Mph. 25: “Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova.” (Ndime 1-10) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Alimbikitseni kuchita chidwi ndi ntchito yowonjezereka ya utumiki wa kumunda panyengo ya Chikumbutso.
Nyimbo Na. 90 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 15: “Ntchito Imene Imatheka Chifukwa cha Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova.” (Ndime 11-17) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Phatikizanipo chitsanzo chachidule cha wofalitsa amene akuchita ulendo wobwereza. Aitanire munthuyo ku Chikumbutso.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya February 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi, ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Chimodzi mwa zitsanzozo chisonyeze mmene tingayankhire mfundo yoletsa kukambirana yakuti “Ndili ndi chipembedzo changa.”—Onani buku la Kukambitsirana, masamba 18-19.
Mph. 15: “Kupezeka Pamisonkhano Nthaŵi Zonse Kukhale Patsogolo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzani pasadakhale zoti mmodzi kapena aŵiri adzafotokoze zimene achita kuti azipezeka pamsonkhano uliwonse wa mpingo.
Mph. 20: Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano.” Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2003, masamba 19-22. (1) Kodi Salmo 22:22, 25 limasonyeza motani chifukwa chimene timaperekera ndemanga pamisonkhano? (2) N’chifukwa chiyani pemphero limathandiza? (3) N’chifukwa chiyani kukonzekera kuli kofunika? (4) Kodi tonsefe tiyenera kukhala ndi cholinga chotani tikakhala pamisonkhano? (5) N’chifukwa chiyani kukhala kutsogolo kuli kothandiza? (6) N’chifukwa chiyani kumvetsera zimene ena akunena kuli kofunika? (7) Kodi tingachite chiyani kuti tiziyankha ndi mawu athuathu? (8) Kodi tingawalimbikitse bwanji ena ndi ndemanga zathu? (9) Kodi wochititsa msonkhano ali ndi udindo wanji?
Nyimbo Na. 81 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 1
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa kumunda a February. Tchulani mabuku ogaŵira mwezi wa March, ndipo kambanipo mwachidule umodzi mwa maulaliki osonyezedwa m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya February 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi, ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Pomaliza chimodzi mwa zitsanzozo, afunse funso lochititsa chidwi limene lingayankhidwe paulendo wotsatira mwa kugwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 15: “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Lengezani tsiku la msonkhano wadera wotsatira. Ngati mpingo udzakhale ndi msonkhano waderawu m’miyezi ingapo ikubwerayi, nenani kuti amene akufuna kubatizidwa auze woyang’anira wotsogolera. Limbikitsani onse kuyesetsa kuitanira ophunzira Baibulo awo kudzapezeka nawo pamsonkhano wonsewu.
Nyimbo Na. 98 ndi pemphero lomaliza.