Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 8
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Chitani zitsanzo zosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya May pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu. M’chitsanzo chimodzi, wofalitsa agawire Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi ya May 15 ndiponso Galamukani! ya May kwa munthu amene amakamugawira magazini nthawi zonse koma amene sanalandire Nsanja ya Olonda ya May 1. Pogawira magazini atatuwo, kambiranani magazini imodzi yokha. Ofalitsa atha kumakapereka magazini kwa anthu amene amalandira magazini nthawi zonse mwina kamodzi kapena kawiri pa mwezi. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph.20: ‘Nditsateni’ Kosalekeza.a Mwachidule funsani wofalitsa wachitsanzo chabwino, amene amayesetsa kukhala ndi moyo wosafuna zinthu zambiri, amenenso amachepetsa zokhumba zake kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu ndi kutumikira ena. Tsindikani za madalitso amene amawapeza pochita zimenezo.
Mph.15: Zokumana nazo mu utumiki. Pemphani omvera kuti afotokoze madalitso amene apeza podzipereka mu utumiki m’miyezi ya March ndi April. Afotokoze zimene akumana nazo poyambitsa maphunziro a Baibulo ndi pothandiza anthu atsopano kufika ku Chikumbutso. Mungachitire chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za zimene zinachitikazo.
Nyimbo Na. 91 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 15
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Kugwira Ntchito Limodzi Mogwirizana Pansi pa Umutu wa Kristu. Nkhani yotengedwa pa kamutu kakuti “Zimene Kuzindikira Ulamuliro Wake Kumatanthauza” m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu pamasamba 14 ndi 15.
Mph.20: “Chititsani Maphunziro a Baibulo Achidule Ndiponso a Patelefoni Opita Patsogolo.”b Chitani chitsanzo chachidule choonetsa zimene wofalitsa anganene pofuna kusintha kuti asiye kuchititsa phunziro lachidule n’kuyamba kuchititsa lalitali.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 22
Mph.12: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka amene alembedwa pa sitetimenti. Chitani zitsanzo zosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu. Zochitika pa zitsanzozo zikhale zoti banja likuyerekezera ulaliki woti likagwiritse ntchito mu utumiki. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph.15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Okoma Mtima ndi Oganizira Ena.”c
Mph.18: Kuoneka Bwino. Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 131 mpaka 133. Kambiranani mfundo zisanu zonena za mmene tiyenera kuvalira ndi kudzikongoletsera. Fotokozani kuti tingathe kugwiritsa ntchito mwaluso mfundo zimenezi kuthandizira ophunzira Baibulo athu kuti azitha kuvala bwino akamabwera ku misonkhano ya mpingo.
Nyimbo Na. 215 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 29
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka lipoti lawo la utumiki wa kumunda la mwezi wa May.
Mph.15: Gawirani buku la Mphunzitsi m’mwezi wa June. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pamasamba 3 ndi 4 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu. Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti afotokoze zotsatira zabwino zimene apeza pogwiritsa ntchito buku limeneli m’munda kapena pabanja pawo.
Mph.20: “Phunzitsani Anthu Ofatsa Kuyenda M’njira ya Mulungu.”d Phatikizaponi ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2004, tsamba 16, ndime 9.
Nyimbo Na. 9 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 5
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: Mmene Tingapangire Maulendo Obwereza Ogwira Mtima. Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa m’bokosi la patsamba 16 la mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2003. Kambiranani iliyonse ya mfundo seveni zimenezi, ndipo pemphani omvera kuti afotokoze mmene angazigwiritsire ntchito kuderako. Limbikitsani ofalitsa kupanga maulendo obwereza n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo ndi aliyense amene walandira mabuku athu kapena amene wasonyeza chidwi. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingapemphere anthu kuti tiyambe kuphunzira nawo Baibulo paulendo wobwereza pogwiritsa ntchito ulaliki umodzi wopezeka patsamba 6 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006.
Nyimbo Na. 57 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.