Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/06 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira August 14
  • Mlungu Woyambira August 21
  • Mlungu Woyambira August 28
  • Mlungu Woyambira September 4
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 8/06 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira August 14

Nyimbo Na. 163

Mph.15: Zilengezo za pampingo. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Lengezani tsiku la msonkhano wapadera wotsatira ngati mukulidziwa. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya August. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene mungachitire ndi munthu amene sakufuna kuti mukambirane naye, amene akunena kuti “Sindili Wokondwera ndi Mboni za Yehova.”—Onani m’buku la Kukambitsirana, mas. 17-18.

Mph.15: “Magazini Yapadera ya Galamukani! Yodzagawira mu September.”a Pokambirana ndime 4, chitani chitsanzo chosonyeza wachinyamata wa zaka zapakati pa 13 ndi 19 akugawira magazini ya Galamukani! ya September kwa mphunzitsi.

Mph.15: Kodi Kucheza ndi Anzanga a ku Sukulu Kumapyola Malire Kukafika Pati? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa mu Galamukani! ya April 2006, kuyambira tsamba 17 mpaka 19. Pemphani omvera amene akulira m’banja lachikristu kuti afotokoze mmene makolo awo anawakonzekeretsera kulimbana ndi zovuta za kusukulu ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Mungathe kukonzekeretseratu munthu mmodzi kapena awiri kuti adzafotokozenso zimenezi.

Nyimbo Na. 164 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 21

Nyimbo Na. 62

Mph.5: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph.10: “Kodi Mumachititsa Phunziro la Baibulo la Banja Nthawi Zonse?” Nkhani yoti ikambidwe ndi mkulu amene amachititsa phunziro la Baibulo ndi banja lake mlungu uliwonse. Werengani ndi kuthirira ndemanga malemba onse amene sanagwidwe mawu onse.

Mph.15: Kupindula ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda Ndiponso Msonkhano wa Onse. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kuyambira tsamba 59 kukalekezera pa kamutu ka patsamba 64.

Mph.15: Yambani Kukonzekera Kudzachita Upainiya Wothandiza. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Limbikitsani omvera kukhala ndi cholinga chodzachita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena ingapo m’chaka chautumiki chikubwerachi. (1 Akor. 9:26) Ena angasankhe mwezi umene uli ndi zochitika zapadera kapena mwezi umene uli ndi masiku atchuthi kapena masiku a Loweruka ndi a Lamlungu ochulukirapo. Funsani omvera kuti: “Kodi munathana bwanji ndi zovuta m’mbuyomu kuti muthe kuchita upainiya wothandiza? Kodi upainiya wothandiza umabweretsa madalitso otani? Ngati mukufuna kuchita upainiya wothandiza koma mukukayikakayika, n’chifukwa chiyani muyenera kupempherera nkhani imeneyi? (Mac. 4:29; 2 Akor. 4:7; Yak. 1:5) N’chifukwa chiyani ndi bwino kukambirana zimenezi ndi anthu apabanja lanu ndi ena mu mpingo wanu, makamaka amene nthawi yawo ndi yanu zingagwirizane? (Miy. 15:22) Kodi inuyo mukukonza zodzachita upainiya wothandiza miyezi iti?”

Nyimbo Na. 216 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 28

Nyimbo Na. 17

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa August. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani chitsanzo chosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya September 1 kapena Galamukani! ya September paulendo wobwereza kwa anthu amene timakawapatsira magazini nthawi zonse.

Mph.15: Mungathe Kulimbikitsa Ena. (Aroma 1:11, 12) Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani chiwerengero cha apainiya okhazikika mu mpingo wanu. Tchulani mmene tingawalimbikitsire, monga kuwayamikira, kunena zabwino zokhazokha za utumiki waupainiya, kuyenda nawo limodzi mu utumiki, kuwaitana kuti mukadye nawo limodzi, kuwapatsako ndalama zoyendera. Pemphani apainiya okhazikika kuti afotokoze mmene ena awalimbikitsira. Ngati mu mpingo wanu mulibe apainiya okhazikika, kambiranani mmene tingalimbikitsire anthu amene amachita upainiya wothandiza.

Mph.20: Kodi Mungathe Kuyambitsa Phunziro la Baibulo mu September? Nkhani ndi zitsanzo. M’mwezi wa September tidzayesetsa mwapadera kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba, pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Zimenezi zikutanthauza kuti tikapatsa mwininyumba bukuli, tiziyesetsa kukambirana naye ndime zingapo. Pogwiritsa ntchito nkhani zoyenererana ndi gawo lanu, khalani ndi zitsanzo ziwiri. M’chitsanzo chilichonse sonyezani mmene tingakonzere kuti tidzabwerenso ndi kupitiriza kukambirana.

Nyimbo Na. 37 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 4

Nyimbo Na. 90

Mph.10: Zilengezo za pampingo.

Mph.15: Zosowa za pampingo.

Mph.20: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kulalikira Mopanda Tsankho.”b Pokambirana lemba la Aroma 1:14, lomwe lili kumapeto kwa ndime 2, fotokozani mwachidule zomwe zili m’buku la Insight, Voliyumu 1, tsamba 255 ndime yoyamba pa mutu wakuti “Barbarian.” Mukatha kukambirana ndime 3, kambiranani mfundo zitatu za patsamba 2, m’kabuku ka Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse. Ndipo chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito kabukuka m’gawo lanu kwa anthu olankhula chinenero china.

Nyimbo 225 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena