Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/06 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira October 9
  • Mlungu Woyambira October 16
  • Mlungu Woyambira October 23
  • Mlungu Woyambira October 30
  • Mlungu Woyambira November 6
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 10/06 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira October 9

Nyimbo Na. 25

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani chitsanzo chosonyeza momwe tingagawire Nsanja ya Olonda ya October 15 ndi Galamukani! ya October, limodzi ndi Uthenga wa Ufumu Na. 37. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: “Thandizani Ena Kukhala Mabwenzi a Mulungu.”a Pemphani omvera kuti alongosole mmene chitsanzo cha ena ndi mapemphero awo ochokera pansi pamtima, zinawathandizira kupita patsogolo mpaka kufika pofuna kubatizidwa.

Mph. 20: Konzekerani Kugawira Uthenga wa Ufumu Na. 37. Nkhani yokambirana ndi omvera. Tchulaninso ndondomeko imene yakonzedwa pa ntchito imeneyi, imene yalongosoledwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September. Limbikitsani onse kuti adzagwire nawo mokwanira ntchito imeneyi. Limbikitsani ofalitsa amene ali ndi maphunziro a Baibulo opita patsogolo kuti aone ngati ophunzirawo angayenerere kudzagwira nawo ntchito imeneyi monga ofalitsa osabatizidwa. Nawonso makolo aone ngati ana awo akuyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa. Tchulani mwachidule ziyeneretso zomwe zili m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova pamasamba 79 mpaka 81.

Nyimbo Na. 221 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 16

Nyimbo Na. 84

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 20: Kupindula ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kuyambira pa kamutu komwe kali pa tsamba 69 mpaka pa kamutu koyamba ka pa tsamba 72.

Mph. 15: “Kodi N’chiyani Chomwe Mumaika Poyamba M’moyo Wanu?”b Pemphani omvera omwe munawasankhiratu kuti alongosole mmene anasinthira zochita zawo kuti aziika zinthu za Ufumu patsogolo, ndipo alongosole madalitso amene apeza chifukwa cha kusinthako.

Nyimbo Na. 172 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 23

Nyimbo Na. 58

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya November. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingayankhire munthu amene akufuna kuti tisakambirane naye ponena kuti “Kodi n’chifukwa ninji anthu inu mumafika mwakawirikawiri.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsa. 20. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: Zosowa za pampingo.

Mph. 20: “Pindulani Mokwanira ndi Misonkhano Yokonzekera Utumiki wa Kumunda.”c Pokambirana ndime yachitatu, phatikizanipo ndemanga zosonyeza mmene zinthu ziyenera kuchitikira ngati palibe abale oyenerera kuti achititse msonkhano umenewu, zochokera pa ndime 4 m’Bokosi la Mafunso la mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2001.

Nyimbo Na. 143 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 30

Nyimbo Na. 207

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda, ndipo kuseri kwa malipotiwo alembe chiwerengero cha Uthenga wa Ufumu Na. 37 umene agawira.

Mph. 15: Kodi Ndingalalikire Bwanji Anzanga a Kusukulu? Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa mu Galamukani! ya April 8, 2002, masamba 14 mpaka 16. Pemphani omvera kuti alongosole zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo polalikira anzawo a kusukulu.

Mph. 20: Zokumana Nazo za Panthawi Yogawira Uthenga wa Ufumu Na. 37. Pemphani ofalitsa kuti alongosole zokumana nazo zolimbikitsa zimene anasangalala nazo pogawira Uthenga wa Ufumu Na. 37. Tchulani za kukula kwa gawo limene mwagwirako kale ntchitoyi, komanso zimene muyenera kuchita kuti mumalize gawo lanu lonse pomafika pa November 12. Chitani chitsanzo chosonyeza kupanga ulendo wobwereza pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kumbutsani ofalitsa kuti abweze Uthenga wa Ufumu umene akuona kuti satha kugawira panthawi ya ntchito yapaderayi kuti anthu ena augwiritse ntchito.

Nyimbo Na. 136 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 6

Nyimbo Na. 146

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, pa tsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani chitsanzo chosonyeza zimene tinganene pogawira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Tidzagawira bukuli kuyambira pakatikati pa mwezi wa November, mpaka kumapeto kwa mweziwu. Ngati nthawi ingalole, pemphani omvera kuti alongosole zinthu zosangalatsa zimene apeza chifukwa chogwiritsa ntchito buku limeneli mu utumiki kapena m’banja lawo.

Mph. 15: Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, masamba 28 mpaka 31.

Mph. 20: Kulalikira Mawu Kumadzetsa Mpumulo. Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2002, tsamba 8 ndi 9. Pemphani omvera kuti alongosole mmene amapezera mpumulo chifukwa cholalikira. Mungakonzeretu zoti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzapereke ndemanga zawo.

Nyimbo Na. 8 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena