Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/06 tsamba 1
  • Kodi N’chiyani Chomwe Mumaika Poyamba M’moyo Wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’chiyani Chomwe Mumaika Poyamba M’moyo Wanu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • “Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 10/06 tsamba 1

Kodi N’chiyani Chomwe Mumaika Poyamba M’moyo Wanu?

1 Kodi mungayankhe bwanji funso limeneli? N’zoona kuti tonsefe timafuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33) Komabe, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosankha zimene ndimapanga zimasonyezadi kuti ndikuchita zimenezi?’ Baibulo limalimbikitsa kuti: “Dziyeseni nokha.” (2 Akor. 13:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kodi ndi motani mmene tingadziyesere tokha kuti tione ngati tikuikadi zinthu za Ufumu patsogolo?

2 Mmene Timagwiritsira Ntchito Nthawi Yathu: Tingayambe ndi kuona mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu. (Aef. 5:15, 16) Mlungu uliwonse, kodi timawononga nthawi yochuluka bwanji pocheza, poonera TV, pogwiritsa ntchito Intaneti, kapena pochita zinthu zina zimene timakonda? Tingadabwe kwambiri ngati titalemba nthawi imene timawononga pochita zinthu zimenezi, ndiyeno n’kuyerekezera ndi nthawi yomwe timathera pochita zinthu zauzimu. Kodi timagwira ntchito kwa maola ena owonjezera n’cholinga choti tipeze ndalama zogulira zinthu zapamwamba, uku tikunyalanyaza utumiki wopatulika? Kodi ndi nthawi zingati zimene timalephera kupita ku misonkhano kapena mu utumiki chifukwa chopita kokasangalala kumapeto kwa mlungu?

3 Chitani Kaye Zinthu Zofunika: Ambirife tilibe nthawi yokwanira yoti tichite zinthu zonse zomwe timafuna. Choncho, kuti tiike zinthu za Ufumu patsogolo, tifunika kusankha zinthu zoti tiziike pamalo oyamba n’kupeza nthawi yoti tichite ‘zinthu zofunika kwambiri.’ (Afil. 1:10 NW) Zinthu zimenezi zimaphatikizapo kuphunzira Mawu a Mulungu, kuchita nawo utumiki, kusamalira banja lathu, ndi kufika pa misonkhano yachikristu. (Sal. 1:1, 2; Aroma 10:13, 14; 1 Tim. 5:8; Aheb. 10:24, 25) Zinthu zinanso monga kuchitako pang’ono zosangalatsa ndiponso masewera olimbitsa thupi n’zothandiza. (Marko 6:31; 1 Tim. 4:8) Koma zinthu zosafunika kwambirizi ziyenera kuikidwa pamalo ake.

4 Mbale wina wachinyamata anaganiza zoika zinthu za Ufumu patsogolo mwa kuyamba utumiki wa nthawi zonse m’malo mopita ku koleji kuti adzapeze ntchito yabwino. Anaphunzira chinenero china ndipo anasamukira kudera komwe kunali Mboni zochepa. Iye anati: “Ndikusangalala kwambiri kuno. Utumiki wake ndi wotsitsimula kwabasi. Ndingasangalale wachinyamata aliyense atachita zinthu ngati zimene ndikuchitazi n’kumva mmene ndikumveramu. Palibenso chinthu china chabwino kuposa kutumikira Yehova ndi mtima wonse.” Zoonadi, kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba kumabweretsa madalitso, ndipo koposa zonse, kumasangalatsa Atate wathu wakumwamba, Yehova.—Aheb. 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena