Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 9
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June.
Mph.20: Kukonzekera Kuchititsa Phunziro la Baibulo. Nkhani yochokera pa tsamba 1 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2004. Kumapeto kwa nkhaniyi, sonyezani chitsanzo cha wofalitsa amene akukonzekera mothamanga kukachititsa phunziro la Baibulo. Kenako sonyezani chitsanzo cha wofalitsa wina amene akukonzekera kukachititsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito ena mwa malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumuwo.
Mph.15: “Lalikirani Mwakhama.”a Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira June 16
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kumbutsani omvera kuti pobwera ku Msonkhano wa Utumiki mlungu wamawa adzatenge Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July ndiponso kuti akakonzekere kudzafotokoza ulaliki umene akufuna kudzagwiritsa ntchito.
Mph.15: Sonyezani Ena Kufunika kwa Uthenga Wabwino. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 159. Pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene anthu a m’gawo lanu akuda nazo nkhawa. Apempheninso kuti atchule zimene akuganiza kuti tinganene mu ulaliki wathu zokhudzana ndi zimene zimadetsa anthu nkhawazo.
Mph.20: “Kodi Banja Lanu Likukonzekera Kupulumuka?”b Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira June 23
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti yochokera ku ofesi. Tchulani mabuku ogawira mu July, ndipo onetsani chitsanzo chimodzi cha kagawiridwe kake.
Mph.20: Upainiya Wokhazikika Umapangitsa Moyo Kukhala Waphindu Kwambiri. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2008, masamba 17 mpaka 19. Ngati n’zotheka, funsani mafunso apainiya awiri okhazikika, mmodzi akhale amene wayamba kumene utumikiwu ndipo winayo akhale amene wachita upainiya zaka zambiri. Afotokoze mmene apindulira pamoyo wawo chifukwa cha utumiki wapadera umenewu.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini Atsopano. Kukambirana ndi omvera. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene zingasangalatse anthu a m’gawo lanu ndipo afotokoze chifukwa chake. Pemphani omvera kuti atchule mfundo zimene akufuna kukatchula m’nkhani zimene akufuna kukagwiritsa ntchito pogawira magaziniwa. Kodi angafunse mafunso ati kuti ayambe kukambirana ndi munthu? Ndi malemba ati m’nkhanizo amene angakagwiritse ntchito? Pogwiritsa ntchito ulaliki wachitsanzo wa mu Utumiki Wathu wa Ufumu kapena mfundo zimene zafotokozedwa ndi omvera, sonyezani chitsanzo cha zimene tingachite pogawira magazini iliyonse.
Mlungu Woyambira June 30
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wakumunda a mwezi wa June.
Mph.20: Mmene Tingakulitsire Luso Lathu Locheza ndi Anthu. Nkhani yokambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 62, ndime 4, mpaka kumapeto kwa tsamba 64. Gwirizanitsani mfundo za m’nkhaniyi ndi gawo lanu. Mwachidule, funsani wofalitsa amene ali ndi luso lotha kuyamba kucheza ndi anthu muulaliki wa nyumba ndi nyumba kapena wamwamwayi.
Mph.15: Kodi Mukukumbukira? Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2008, tsamba 29.
Mlungu Woyambira July 7
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Zimene Tingachite Tikapeza Mwininyumba Wolankhula Chinenero China.”c Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pokambirana ndime 2, dziwitsani mpingo za magulu kapena mipingo ya zinenero zina imene ikulalikiranso m’dera limene mpingo wanu umalalikira. Fotokozani dongosolo lililonse lofunika kutsatira n’cholinga chothandiza magulu kapena mipingo ya zinenero zinayo kuti ntchito yolalikira iyende bwino.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.