Kodi Banja Lanu Likukonzekera Kupulumuka?
1 Maulosi a m’Baibulo omwe akwaniritsidwa akupereka umboni wamphamvu wakuti mapeto a dziko loipali ali pafupi. Zochitika za m’nthawi yathu ino n’zofanana kwambiri ndi za m’nthawi ya Nowa, Chigumula chisanachitike. (Mat. 24:37-39) Chifukwa chakuti Nowa “anayendabe ndi Mulungu,” iye anapulumuka pamene anthu a m’nthawiyo anawonongedwa. (Gen. 6:9) N’zosakayikitsa kuti Nowa anaphunzitsa banja lake zinthu zimene Yehova amafuna. Tikutero chifukwa chakuti banja lake nalonso linapulumuka. Kodi ife tingam’tsanzire motani Nowa n’kukonzekera monga banja kuti tidzapulumuke mapeto a dongosolo loipali la zinthu?
2 Mlaliki wa Chilungamo: Nowa anapirira pantchito yake ndipo anakhala “mlaliki wa chilungamo” mwina kwa zaka 40 kapena 50. (2 Pet. 2:5) Mosakayikira, anthu oyandikana naye ankamunyoza chifukwa cha ntchito yake yolalikira. Mwina anthuwo ankachita zimenezo chifukwa chotengera angelo opanduka omwe anasintha matupi awo n’kukhala ngati anthu. Nthawi zambiri anthu sakhala ndi chidwi ndi uthenga wathu ndipo amanyoza. Zimenezi zikutsimikizira kuti mapeto a dongosolo ili la zinthu ayandikira. (2 Pet. 3:3, 4) Komabe, mosiyana ndi anthu a m’nthawi ya Nowa, masiku ano anthu ambiri akumvera uthenga umene timalalikira ndipo ‘akusonkhana’ kuti alambire Yehova. (Yes. 2:2) Ngati titapirira, tidzapulumuka ndipo nawonso anthu otimvera adzapulumuka. (1 Tim. 4:16) Motero, m’pofunika kwambiri kuti makolo aphunzitse ana awo kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuigwira mwachangu. Ndipo makolowo ayenera kutero mwa zolankhula zawo ndiponso zochita zawo.—2 Tim. 4:2.
3 “Momwemo Anachita”: Nowa ndi banja lake anapulumuka chifukwa choti anatsatira bwinobwino malangizo a Yehova. (Gen. 6:22) Kuti ifenso tidzapulumuke, m’pofunika kuti tikhale ‘okonzeka kumvera’ malangizo a m’Baibulo ndiponso a kapolo wokhulupirika. (Yak. 3:17) Mwachitsanzo, bambo wina anatsatira malangizo a gulu la Yehova ndipo ankachititsa phunziro la banja ndiponso ankapita ndi banja lake muutumiki wakumunda mlungu uliwonse. Ndipo iye ankayesetsa kuti mlungu uliwonse asamangoyenda ndi mwana mmodzimodzi muutumiki. Khama lake pochita zimenezi linalimbikitsa ana ake onse 6 moti anakhala atumiki okhulupirika a Yehova.
4 Mapeto a dongosolo lino la zinthu adzafika mwadzidzidzi. (Luka 12:40) Tikatsatira chitsanzo cha Nowa ndiponso kukhulupirira njira yotipulumutsira imene Mulungu wakonza, ifeyo ndiponso banja lathu tidzakhala okonzeka.—Aheb. 11:7.