Ndandanda ya Mlungu wa June 15
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 15
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 21 ndime 1-8
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 6-9
Na. 1: Levitiko 8:1-17
Na. 2: ‘Kodi Mumakhulupirira za Machiritso?’ (rs-CN tsa. 170 ndime 3 ndi 4)
Na. 3: Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza (lr-CN mutu 22)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Lalikirani Uthenga Wabwino. Nkhani yolimbikitsa yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 279, ndime 1 mpaka 4.
Mph.10: Ngati Wina Anena Kuti, ‘Ndimakhulupirira Chisinthiko.’ Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Kukambitsirana, patsamba 104 ndi 105. Phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayankhire ngati wina akunena kuti, ‘Ndimakhulupirira kuti Mulungu analenga munthu kupyolera mwa chisinthiko.’
Mph.10: “Konzekerani Bwino Pokaphunzitsa.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.