Konzekerani Bwino Pokaphunzitsa
1. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kumvetsa choonadi?
1 Tikamachititsa phunziro la Baibulo, tiyenera kukonzekera bwino kuti tithandize wophunzirayo kutumikira Yehova. Kuti zimenezi zichitike, tiyenera kuyesetsa kuthandiza wophunzira kumvetsa bwino zimene akuphunzira m’Baibulo. (Deut. 6:5; Miy. 4:23; 1 Akor. 9:26) Kodi tingachite bwanji zimenezi?
2. Kodi pemphero lingatithandize bwanji pokonzekera phunziro?
2 Muzipemphera Pokonzekera: Popeza kuti Yehova ndi amene amakulitsa mbewu ya choonadi mu mtima wa wophunzira, ndi bwino kuti poyamba kukonzekera phunziro tizipempherera munthuyo komanso zimene akufunikira. (1 Akor. 3:6; Yak. 1:5) Pemphero loterolo lingatithandizenso kudziwa zimene tingachite kuti timuthandize kudzaza mu mtima wake zinthu ‘zolondola’ zokhudza chifuniro cha Yehova.—Akol. 1:9, 10.
3. Kodi tingakonzere bwanji phunziro moganizira wophunzira wathu?
3 Ganizirani Wophunzirayo: Yesu ankadziwa kuti kuphunzitsa mogwira mtima kumaphatikizapo kuganizira anthu amene tikuwaphunzitsa. Maulendo awiri, Yesu anafunsidwa kuti: “Ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” Maulendo onsewa, Yesu anayankha mosiyana. (Luka 10:25-28; 18:18-20) Choncho, tiyenera kuganizira wophunzira wathu pamene tikukonzekera phunziro. Kodi ndi Malemba ati osagwidwa mawu amene tikawerenge naye? Kodi tikaphunzira naye zinthu zochuluka bwanji? Kodi ndi mfundo ziti m’phunzirolo zimene zingamuvute wophunzira wanga kuzimvetsa kapena kuzikhulupirira? Kuganizira mafunso ena amene wophunzira wathu angafunse, kumathandiza kuti tikhale okonzeka kuwayankha mogwira mtima.
4. Kodi kukonzekera bwino kumaphatikizapo kutani?
4 Konzekerani Zimene Mukukaphunzitsa: Zilibe kanthu kuti taphunzira nkhaniyo kangati, koma kwa munthu amene tikuphunzira nayeyo imakhala nthawi yake yoyamba. Ngati tikufuna kumufika pamtima wophunzira wathu, tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse. Zimenezi zikutanthauza kuti ifenso tiyenera kuchita zimene timalimbikitsa wophunzira wathu kuti azichita. Werengani zimene mukukaphunzitsa, kuphatikizapo Malemba amene sanagwidwe mawu, moganizira wophunzira wanuyo ndiponso mwina kudula mizere kunsi kwa mfundo zazikulu.—Aroma 2:21, 22.
5. Kodi tingamutsanzire bwanji Yehova?
5 Yehova amasangalala kwambiri wophunzira Baibulo aliyense akamapita patsogolo. (2 Pet. 3:9) Tikamakhala ndi nthawi yokonzekera phunziro lililonse, timasonyeza kuti ifenso timasangalala.