Ndandanda ya Mlungu wa June 22
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 22
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 21 ndime 9-15
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 10-13
Na. 1: Levitiko 11:29-45
Na. 2: Chifukwa Chake Anthufe Timadwala (lr-CN mutu 23)
Na. 3: Madalitso Amene Ophunzira Obatizidwa Amapeza
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Thandizani Omvera Anu Kugwiritsa Ntchito Luso la Kuzindikira. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 57, ndime 3 mpaka tsamba 58, ndime 3.
Mph.10: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili m’magaziniwo, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene akufuna kudzagwiritsira ntchito m’gawo lawo ndiponso chifukwa chake. Kodi angagwiritsire ntchito mafunso ndi Malemba otani posonyeza nkhanizo? Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse.
Mph.10: Mmene Mungayankhire Anthu Amene Akukana Kukambirana za Chipembedzo. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Kukambitsirana, patsamba 91 ndime 3, mpaka tsamba 94 ndime 2. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri pogwiritsa ntchito malangizo a m’bukulo.