Ndandanda ya Mlungu wa June 29
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 29
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 21 ndime 16-21 ndi bokosi la patsamba 217
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 14-16
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Kuoneka Bwino—Chifukwa Chake N’kofunika. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 131 mpaka 134.
Mph.10: Sankhani Nkhani za M’Baibulo Zoyenera “Anthu Osiyanasiyana.” (1 Akor. 9:22) Kukambirana ndi omvera. Mukatha kukambirana mafunso otsatirawa, omvera angafotokoze zimene anakumana nazo. Kodi ndi nkhani ziti zimene mwaona kuti n’zosangalatsa anthu a misinkhu inayake, akazi kapena amuna, kapenanso achipembedzo chinachake? Kodi tingagwiritse ntchito bwanji buku la Kukambitsirana posankha nkhani zimene zingasangalatse anthu osiyanasiyana? Kodi tingachite chiyani kuti tisonyeze kulolera ngati mwininyumba wasankha kuti tikambirane nkhani yosiyana ndi imene takonzekera?
Mph.10: Mabuku Ogawira mu July ndi August. Fotokozani zimene zili m’mabukuwo. Chitani zitsanzo ziwiri kapena zitatu za maulaliki amene angakhale ogwira mtima m’gawo lanu.