Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
1. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa lamulo lopezeka pa Eksodo 23:19? [w06-CN 4/1 tsa. 31 ndime 1 mpaka 5]
2. Kodi Urimu ndi Tumimu zinali chiyani, ndipo zinkagwiritsidwa ntchito motani m’nthawi ya Isiraeli? (Eks. 28:30) [w06-CN 1/15 tsa. 18; w01-CN 9/1 tsa. 27]
3. Kodi Yehova analankhula motani ndi Mose “kopenyana maso”? (Eks. 33:11, 20) [w04-CN 3/15 tsa. 27]
4. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Aisiraeli amene anapereka zinthu ndi kugwiritsa ntchito luso lawo pomanga chihema? (Eks. 35:5, 10) [w99-CN 11/1 tsa. 31 ndime 1 ndi 2]
5. Kodi nsalu yotsekera imene ikutchulidwa pa Eksodo 40:28 imaimira chiyani m’kachisi wauzimu wamkulu wa Mulungu? [w00-CN 1/15 tsa. 15 ndime 7 ndi 8]
6. Kodi “nsembe yopsereza” imene inkaperekedwa yonse imafanana bwanji ndi nsembe ya Yesu? (Lev. 1:13) [w04-CN 5/15 tsa. 21 ndime 3]
7. Kodi mfundo yakuti “mafuta onse nga Yehova” ikutiphunzitsa chiyani? (Lev. 3:16, 17) [w04-CN 5/15 tsa. 22 ndime 2]
8. Kodi kuthira mwazi patsinde pa guwa lansembe ndi kuupaka pa zipangizo zosiyanasiyana kunali ndi tanthauzo lanji? [w04-CN 5/15 tsa. 22 ndime 5]
9. Kodi lemba la Levitiko 12:8 likutiuza chiyani za makolo a Yesu, ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? [w98-CN 12/15 tsa. 6 ndime 5]
10. Kodi ntchito ya nsembe ya dipo ya Yesu inaphiphiritsiridwa motani pa Tsiku Lachitetezo la chaka ndi chaka la Isiraeli? (Lev. 16:11-16) [w98-CN 2/15 tsa. 12 ndime 2]