‘Uthenga Wabwino Uwu Udzalalikidwa’
1. Kodi tikudziwa bwanji kuti palibe chilichonse chimene chingalepheretse ntchito yolalikira?
1 Palibe chilichonse chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa chifuniro chake. (Yes. 14:24) Ngakhale kuti zinkaoneka ngati n’zosatheka kuti Oweruza Gideoni ndi asilikali ake 300 agonjetse asilikali a ku Midiyani okwana 135,000, Yehova anamuuza kuti: ‘Udzapulumutsa Isiraeli m’dzanja la Midyani. Sindinakutuma ndine kodi?’ (Ower. 6:14) Kodi ndi ntchito iti imene Yehova akuichirikiza masiku ano? Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Palibe aliyense amene angalepheretse ntchito imeneyi.
2. N’chifukwa chiyani tingayembekezere kuti Yehova angatithandize ifeyo patokha mu utumiki?
2 Yehova Amatithandiza Aliyense Payekha: Sitikayika kuti Yehova amathandiza Mboni zake monga gulu, komano kodi tiyenera kuyembekezera kuti iye angatithandizenso aliyense payekha? Panthawi imene Paulo ankafunikira kwambiri kulimbikitsidwa, iye anaona kuti Yehova wamuthandiza pogwiritsira ntchito Mwana wake Yesu. (2 Tim. 4:17) Nafenso tisamakayike kuti Yehova angadalitse zimene aliyense wa ife amachita pokwaniritsa chifuniro chake.—1 Yoh. 5:14.
3. Kodi Yehova amatithandiza pa zinthu zotani?
3 Kodi mumalefuka ndi nkhawa za tsiku ndi tsiku moti simukhala ndi mphamvu zochitira utumiki? ‘Yehova amawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.’ (Yes. 40:29-31) Kodi mukuzunzidwa kapena kutsutsidwa? ‘Mum’senze Yehova nkhawa zanu, ndipo Iye adzakugwirizizani.’ (Sal. 55:22) Kodi nthawi zina mumadzikayikira? ‘Mukani, ndipo Ine ndidzakhala m’kamwa mwanu.’ (Eks. 4:11, 12) Kodi muli ndi vuto kapena matenda enaake amene amakulepheretsani kuchita zambiri mu utumiki? Yehova angathe kudalitsa zinthu zochepa zimene mungachite ndi mtima wanu wonse. Iye amayamikira kwambiri zimenezi.—1 Akor. 3:6, 9.
4. Kodi kudalira Yehova kungatithandize bwanji?
4 Dzanja la Yehova “latambasulidwa, ndani adzalibweza?” (Yes. 14:27) Sitikayika kuti Yehova amadalitsa utumiki wathu, choncho tiyeni tipitirize kulalikira “molimba mtima mwa mphamvu ya Yehova.”—Mac. 14:3.