Ndandanda ya Mlungu wa July 19
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 19
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 9, ndime 22-26 ndi bokosi patsamba 109; Zakumapeto, kuyambira pakamutu patsamba 218-219a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 12-14
Na. 1: 1 Mafumu 12:12-20
Na. 2: Kodi N’chiyani Chingatithandize Kuti Tiziona Abale Athu Mmene Yehova Amawaonera?
Na. 3: Tetezani Ubwenzi Wanu ndi Yehova, Ndipo Pewani Mayanjano Oipa (rs tsa. 172 ndime 2)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 8: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Gawo 2. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 112, ndime 3, mpaka tsamba 114, ndime 1. Funsani mpainiya mmodzi kapena apainiya awiri ndipo afotokoze zimene anasintha pa moyo wawo kuti athe kuchita upainiya.
Mph. 12: “Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo.” Kambiranani ndi omvera. Limbikitsani onse kubweretsa chakudya m’malo mochoka pamalo amsonkhano kukagula chakudya kwa amene ayala malonda pamsewu kapena kumalesitilanti.
Mph. 10: “Kodi Ndikuchita Zokwanira?” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
[Mawu a M’munsi]
a Mungasankhe kuwerenga bokosi kapena Zakumepeto.