Nkhani Zatsopano Zoyambitsira Maphunziro A Baibulo
1. Kodi Nsanja ya Olonda yogawira izikhala ndi nkhani zatsopano zotani, nanga cholinga cha nkhanizi ndi chotani?
1 Kuyambira mwezi wamawa, magazini ya Nsanja ya Olonda yogawira izikhala ndi nkhani zimene zizitithandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Nkhanizi zizikhala ndi mutu wakuti “Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena.” N’zodziwikiratu kuti ena m’dera lathu adzasangalala kuwerenga nkhani iliyonse, koma cholinga cha nkhanizi n’choti tizizigwiritsa ntchito pokambirana ndi mwininyumba.
2. Kodi m’nkhanizi muzikhala zotani?
2 Kodi Muzikhala Zotani?: Mutu waukulu komanso timitu tating’ono tizilembedwa mwa mafunso oti tizifunsa mwininyumba pokambirana. Malemba amene akugwirizana kwambiri ndi nkhaniyo sanawagwire mawu kuti mwininyumbayo akhale ndi mwayi wowerenga yekha kuchokera m’Mawu a Mulungu. Ndime zake ndi zazifupi n’cholinga choti zizikhala zotheka kukambirana ndi mwininyumba muli chiimire. Nkhani iliyonse ikulozera ku buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuti tisamavutike ngati tikufuna kuyamba kukambirana naye pogwiritsa ntchito bukuli.
3. Tikamalalikira khomo ndi khomo, kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhanizi kuti tiyambitse phunziro la Baibulo?
3 Mmene mungagwiritsire ntchito nkhanizi: Pogawira magazini mungafunse funso limene lingachititse chidwi mwininyumba lokhudza mfundo yaikulu ya nkhaniyo. Mwachitsanzo, nkhani imene ili m’magazini ya January 1 ikusonyeza kufunika kwa Baibulo. Mungamufunse kuti: “Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu kapena kuti langokhala buku labwino basi? [Yembekezani ayankhe.] Ndili ndi mfundo inayake yochititsa chidwi pa nkhani imeneyi.” Musonyezeni funso loyamba, kenako werengani ndime yoyamba ndi lemba lake. Werenganinso funsolo ndipo pemphani mwininyumbayo kuti apereke ndemanga yake. Mungaone nokha kuchuluka kwa zimene mungakambirane, ndipo mungagwiritse ntchito mafunso okhala ndi manambala ngati mfundo zoyenera kukambirana. Musanachoke, funsani funso lotsatira ndipo gwirizanani nthawi imene mungakwanitse kudzabweranso kuti mudzakambirane funsolo. Bwereraniko mlungu uliwonse kuti mukakambirane nkhani zotsalazo mpaka pamene mudzalandire magazini ya mwezi wotsatira. Njira ina ndi yongofikira kupempha mwininyumba kuti muyambe kuphunzira naye Baibulo. Mungagwiritse ntchito nkhani imene ili m’magaziniyo pomuonetsa mmene mumaphunzirira Baibulo.
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhanizi popanga maulendo obwereza?
4 Mungagwiritsenso ntchito nkhanizi kwa anthu amene mumawagawira magazini komanso popanga maulendo obwereza. Mukhoza kungonena kuti: “Nsanja ya Olonda yayamba kukhala ndi nkhani zatsopano. Ndingakonde kukuonetsani mmene mungagwiritsire ntchito nkhani zimenezi.” Ndi pemphero lathu kuti nkhani zimenezi zithandiza anthu ambiri ‘kudziwa choonadi molondola.’—1 Tim. 2:4.