Ndandanda ya Mlungu wa December 27
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 27
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 25-28
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. “Kalendala ya 2011 ikutsindika kufunika kwa Kulambira kwa pabanja.” Nkhani.
Mph. 10: Kodi Kukhala ndi Autilaini mu Utumiki N’kothandiza Bwanji? Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki masamba 167 mpaka 168, ndime 1. Pogwiritsa ntchito magazini ya mwezi wotsatira, sonyezani wofalitsa akulankhula yekha kwa mphindi zingapo pokonzekera zimene akanene mu utumiki.
Mph. 10: Imvi Ndizo Chisoti Chachifumu cha Ulemerero. (Miy. 16:31) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2005, tsamba 8-9. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene ayenera kuonera anthu okalamba a mu mpingo.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa January. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani mitu iwiri kapena itatu, ndipo funsani omvera kuti afotokoze mafunso ndiponso malemba amene akhoza kugwiritsa ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse.