Kalendala ya 2011 Ikutsindika za Kulambira kwa Pabanja
Mfundo yaikulu ya Kalendala ya 2011 ya Mboni za Yehova ndi yokhudza Kulambira kwa Pabanja. Kalendalayi ili ndi zithunzi za mabanja a masiku ano ndi mabanja a m’nthawi za Baibulo. Kalendalayi ikusonyezanso atumiki a Yehova okwatira ndi osakwatira akuphunzira Mawu ake.
Anthu a m’Baibulo amene akusonyezedwa m’kalendalayi ankakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo zimenezi zinawathandiza kwambiri kupirira mavuto amene ankakumana nawo. (Sal. 1:2, 3) Tikamaona chithunzi chilichonse cha pakalendalayi tizikumbutsidwa za kufunika kochita Kulambira kwa Pabanja, kaya banja lathu ndi lalikulu kapena laling’ono, komanso kaya m’banjamo tonse ndife Mboni kapena ena si Mboni. Kalendalayi ili ndi malo oti mulembepo tsiku limene banja lanu linakonza kuti muzichita Kulambira kwa Pabanja. Kodi inuyo mwalemba kale tsiku limeneli pakalendala yanu?