Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa December: Gawirani buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati pakhomopo pali ana mungagawire buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. January 2011: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli, mungamugawire buku lililonse limene linatuluka chaka cha 1995 chisanafike. Mu February 2011 ndi March 2011: gawirani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kapena lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuti muyambitse phunziro la Baibulo.
◼ Chikumbutso cha mu 2012 chidzachitika Lachinayi, pa April 5, dzuwa litalowa.