Zochitika mu Utumiki Wakumunda
N’zosangalatsa kwambiri kuona mmene Yehova akudalitsira ntchito yathu muno m’Malawi. Tsopano tili ndi mipingo 1,235 ndiponso timagulu takutali tokwana 19. Ndipo mu March, mwezi womwe tinali ndi Chikumbutso, ofalitsa ambiri anawonjezera nthawi imene amathera mu utumiki wakumunda. Chifukwa cha zimenezi tinathera maola okwana 1,208,954 polalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso kupanga ophunzira atsopano. Tinagawira magazini okwana 424,461 komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo okwana 82,797. Kuwonjezera pa zimenezi, tamaliza kumanga Nyumba za Ufumu zoposa 1,000 m’gawo la nthambi yathu ndipo nyumba zimenezi zikugwiritsidwa ntchito pa kulambira koyera.