Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/10 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Zimene Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 12/10 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda December 1

“Kodi mukuvomereza kuti makolo amene sali pabanja amakumana ndi mavuto ambiri kuposa makolo amene ali pabanja? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatilimbikitsa kuchita zinthu moganizira anthu amene amakumana ndi mavuto. [Werengani Salimo 41:1.] Nkhani imene ikuyambira patsamba 22 ikufotokoza zimene tingachite posonyeza kuti timaganizira makolo amene sali pabanja.”

Galamukani! December

“Anthu ambiri amakhala ndi funso lakuti, ‘Ngati kuli Mulungu, bwanji samangomuwononga Mdyerekezi?’ Kodi inuyo munayamba mwadzifunsapo funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani yomwe ili patsamba 10 ndi 11 ikuyankha funso limeneli pogwiritsa ntchito Baibulo. Ikutiuzanso mmene dzikoli lidzakhalire Mdyerekezi akadzawonongedwa.” Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.

Nsanja ya Olonda January 1

“Anthu ambiri amakhulupirira kuti nkhani yokhudza munda wa Edeni ndi nthano chabe. Kodi mukudziwa kuti Yesu analankhulapo za Adamu ndi Hava monga anthu enieni? [Yembekezani ayankhe. Ndipo kenako werengani Mateyu 19:4-6.] Magazini iyi ili ndi mayankho amafunso ena amene anthu ambiri amakhala nawo okhudza munda wa Edeni.”

Galamukani! January

Aonetseni chikuto cha magaziniyo kenako n’kuwafunsa kuti, “Kodi mungayankhe bwanji funso ili? [Yembekezani ayankhe.] Malemba amalimbikitsa anthu kuti azikhala amtendere. [Werengani Yakobo 3:17.] Ndiye nanga n’chifukwa chiyani chipembedzo chalephera kugwirizanitsa anthu? Kodi tiyembekezere kuti zipembedzo zidzathandiza kuti anthu azikhala mwamtendere? Magazini iyi ikutithandiza kupeza mayankho amafunso amenewa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena