Ndandanda ya Mlungu wa April 25
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 25
Nyimbo Na. 14 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 6 ndime 1-9 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yobu 33-37 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. “Agwiritseni Ntchito, Osati Kungowasunga.” Nkhani. Uzani omvera za mabuku alionse akale amene aunjikana pa mpingopo.
Mph. 10: “Lipoti la Chaka Chautumiki cha 2010.” Nkhani yokambirana yochokera pa Lipoti la Chaka Chautumiki cha 2010. Fotokozani mbali zimene zinapita patsogolo kwambiri pa ntchito yathu yolalikira padziko lonse m’chaka chautumiki chapitachi.
Mph. 20: “Kulambira kwa Pabanja N’kofunika Kwambiri Kuti Tidzapulumuke.” Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2009, tsamba 29-31. Funsani abale awiri omwe ndi mitu ya mabanja. Abalewo akhale amene amachititsa Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse m’mabanja mwawo. Afotokoze mmene mabanja awo apindulira chifukwa chochita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse.
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero