Ndandanda ya Mlungu wa May 30
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 30
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 7 ndime 17-21 ndi bokosi patsamba 75 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 26-33 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 31:9-24 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Anthu Otchulidwa M’Baibulo Amene Anasonyeza Kudzichepetsa Kwenikweni (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ayuda Ayenera Kukhulupirira Yesu Kuti Adzapulumuke?—rs tsa. 44 ndime 3 ndi 4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyamba m’mwezi wa June. Limbikitsani onse kuti ayesetse kuyambitsa maphunziro.
Mph. 15: Mmene Mungafufuzire. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 33 mpaka 38. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha pofufuza m’mabuku athu yankho la funso limene wafunsidwa mu utumiki.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa June. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, tchulani nkhani zina zimene zili m’magaziniwo. Kenako sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu, ndipo funsani omvera kuti anene mafunso ndi malemba amene tingagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero