Kodi Yehova Amaona Chiyani mwa Ife?
1. Tchulani makhalidwe ena amene Yehova amasangalala nawo mwa anthu akamasanthula mitima.
1 Baibulo limatiphunzitsa zinthu zimene Yehova amaziona kukhala zofunika kwambiri mwa atumiki ake. Kunena mosapita m’mbali, iye amakondwera ndi makhalidwe athu abwino ndiponso khama lathu. Mfumu Davide inauza mwana wake Solomo kuti: “Yehova amasanthula mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9) Pamene Mulungu akusanthula mitima ya anthu miyandamiyanda m’dziko lino lodzala ndi chiwawa ndi chidani, ayenera kuti amasangalala kwambiri akapeza mtima umene umakonda mtendere, choonadi ndi chilungamo. Kodi chimachitika n’chiyani Mulungu akapeza munthu amene mtima wake umakonda kwambiri Mulunguyo, amene amafuna kuphunzira za iye ndiponso kuuzako ena zimene akuphunzirazo? Yehova akutiuza kuti amadziwa anthu amene amauzako ena za iye. Ndipotu iye ali ndi “buku la chikumbutso” la onse ‘oopa Yehova ndi anthu amene amaganizira za dzina lake.’ (Mal. 3:16) Makhalidwe amenewa ndi amtengo wapatali kwa iye.
2. Tchulani ntchito zina zimene timagwira zomwe Yehova amaziona kuti ndi zamtengo wapatali.
2 Kodi ndi ntchito zina ziti zabwino zimene Mulungu amaziwerengera? Mosakayikira, amaona khama limene timachita potsanzira Mwana wake, Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Ntchito ina yofunika kwambiri imene Mulungu amawerengera ndi yofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wake. Pa Aroma 10:15, timawerenga kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwabasi!” Popeza kuti mwachibadwa sitingaganizire zoti mapazi athu ndi “okongola,” ndiye kuti palembali mawuwa akuimira khama limene atumiki a Yehova amachita polalikira uthenga wabwino. Khama limeneli ndi lamtengo wapatali kwa Mulungu.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
3. N’chifukwa chiyani tinganene motsimikiza kuti Yehova amawerengera kupirira kwathu tikamakumana ndi mavuto osiyanasiyana?
3 Khalidwe lina limene Yehova amawerengera ndi la kupirira. (Mat. 24:13) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Satana amafuna kuti musamamvere Yehova. Tsiku lililonse limene mwakhala wokhulupirika kwa Yehova mumakhala mukuthandizira Mulungu kupeza choyankha Satana amene ndi wotonza. (Miy. 27:11) Nthawi zina kupirira kumakhala kovuta kwambiri. Matenda, mavuto a zachuma, nkhawa, ndi zopinga zina zingapangitse tsiku lililonse limene likudutsa kukhala loyesa chikhulupiriro. Nthawi zina timakhumudwanso ngati zinthu zimene takhala tikuyembekezera zalephereka. (Miy. 13:12) Tikamapirira pamene tikukumana ndi mayesero ngati amenewa timakhala amtengo wapatali kwa Yehova. N’chifukwa chake Mfumu Davide inapempha Yehova kuti asunge misozi yake ‘m’thumba lachikopa.’ Kenako anafunsa ali ndi chikhulupiriro kuti: “Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?” (Sal. 56:8) Inde, Yehova amasunga mosamala kwambiri ndipo amakumbukira misozi yonse ndi kuvutika kumene tapirira pamene tikupitiriza kukhala okhulupirika kwa iye. Zimenezinso ndi zamtengo wapatali pamaso pake.
4. Kodi Yehova sakhala ndi maganizo olakwika ati kwa atumiki ake okhulupirika?
4 Mtima wathu wodzitsutsa ungakane umboni wakuti Mulungu amatiwerengera. Nthawi zonse ungamanene chapansipansi kuti: ‘Komatu pali anthu ena ambiri achitsanzo chabwino kuposa ineyo. Yehova ayenera kuti amakhumudwa kwambiri akandiyerekezera ndi anthu amenewo.’ Yehova sayerekeza anthu. Iye amatha kusintha maganizo ndipo si wouma mtima. (Agal. 6:4) Iye amasanthula mitima mwanzeru kwambiri ndipo amawerengera khalidwe labwino ngakhale litakhala laling’ono kwambiri.