Ndandanda ya Mlungu wa April 2
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 2
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 4, bokosi lokha patsamba 33 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 17-21 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 21:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ulamuliro wa Satana Watsimikizira Mfundo Iti? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Chimene Chingathandize Kuti Banja Liziyenda Bwino N’chiyani?—rs tsa. 388 ndime 1-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba lino, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro Loweruka loyambirira m’mwezi wa April.
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa April. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri fotokozani nkhani zochepa zimene zili m’magaziniwo zimene zingakhale zothandiza m’gawo la mpingo wanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero