Ndandanda ya Mlungu wa March 26
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 26
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 4 ndime 1-4 ndi bokosi patsamba 30 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 12-16 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 13:1-14 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ndani Ali Oyenerera Kudya pa Mgonero wa Ambuye?—rs tsa. 72 ndime 3-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Uyenera Kuchitika Liti Ndiponso Kangati?—rs tsa. 73 ndime 2 mpaka tsa. 74 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Dziwitsani mpingo magawo amene atsala kuti mugawireko timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso.
Mph. 10: Musaiwale Kuchereza Alendo. (Aheb. 13:1, 2) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Kambiranani zimene mpingo wakonza zokhudza Chikumbutso. Fotokozani njira zothandiza zimene aliyense angatsatire kuti adzalandire bwino alendo ndiponso ofalitsa ofooka amene adzabwere pa Chikumbutso. Chitani chitsanzo chachidule cha mbali ziwiri. Poyamba, sonyezani wofalitsa akulandira munthu amene analandira kapepala koitanira anthu mwambowu usanayambe. Kenako mwambowu utatha, sonyezani wofalitsayo akukonza zoti adzakumanenso ndi mlendoyo kuti adzalimbikitse chidwi chake.
Mph. 20: “Kodi Yehova Amaona Chiyani mwa Ife?” Mafunso ndi mayankho. Kambiranani mmene mfundo za m’nkhaniyi zingatithandizire kuti tizichitirana zinthu moganizirana.
Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero