Ndandanda ya Mlungu wa June 18
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 18
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 7 ndime 14-18 ndi mabokosi patsamba 57 ndi 58 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Maliro 3-5 (Mph. 10)
Na. 1: Maliro 5:1-22 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mungayankhe Bwanji Ngati Wina Atakufunsani Kuti, ‘Kodi Mumakhulupirira Namwali Mariya?’—rs tsa. 260 ndime 4–tsa. 261 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Timakhulupirira Kuti Baibulo Analiuzira Ndi Mulungu?—2 Tim. 3:16 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Bokosi la Mafunso. Nkhani.
Mph. 10: Kodi Mukukumbukira? Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 32.
Mph. 15: Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano.” Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2003, masamba 19-22. (1) Mogwirizana ndi lemba la Salimo 22:22, 25, n’chifukwa chiyani timafunika kuyankha pamisonkhano? (2) N’chifukwa chiyani kukonzekera misonkhano n’kofunika kwambiri? Kodi tonsefe tiyenera kukhala ndi cholinga chotani tikakhala pamisonkhano? (3) N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kumamvetsera pamene ena akuyankha? (4) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyankha mosachita kuwerenga zimene zalembedwa pandime? (5) Kodi tingalimbikitse bwanji ena ndi mayankho athu? (6) Kodi wokamba nkhani ya mafunso amakhala ndi udindo wotani?
Nyimbo Na. 24 ndi Pemphero